Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
1. Ndi buku liti limene tidzayamba kuphunzila pa Phunzilo la Baibulo la Mpingo kuyambila mlungu wa October 19?
1 Kuyambila mlungu wa October 19, 2015, tidzayamba kuphunzila buku lakuti Tsanzirani chikhulupiriro chawo pa Phunzilo la Baibulo la Mpingo. Bukuli likufotokoza nkhani za amuna ndi akazi 14 acikhulupililo ochulidwa m’Baibulo. Likufotokoza m’njila yakuti tizitha kuona anthu okhulupilika amenewa m’maganizo mwathu, ndi kuona mavuto amene anakumana nao potumikila Yehova. Bukuli likufotokozanso zimene tikuphunzilapo pa nkhani zimenezi.—Aheb. 6:12.
2. Fotokozani zinthu zina zimene zili m’buku la Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo.
2 Zimene zili m’Bukuli: Buku limeneli lionetsa nthawi imene zinthu zinacitika, mamapu otithandiza kudziŵa kumene munthu wochulidwayo anali kukhala ndi panthawi imene anakhalapo. Kuonjezela apo, mutu uliwonse uli ndi kamutu kakuti, “Mfundo Zofunika Kuziganizira . . . ,” kamene kadzatithandiza kusinkhasinkha ndi kuseŵenzetsa zimene taphunizila. Bukuli, lilinso ndi zithunzi zambili zokongola zimene zidzatithandiza kuganizila nkhaniyo.
3. Tingacite ciani kuti tipindule pophunzila buku limeneli?
3 Zimene Tingacite Kuti Tipindule: Kalata yocokela ku Bungwe Lolamulila imene ili m’bukuli, ili ndi mau olimbikitsa awa: “Pamene mukuŵelenga, yelekezelani kuti zinthuzo zikucitika inu muli pomwepo ndipo muziganizila mmene zinthu zochulidwa m’nkhaniyo zinkaonekela, kumvekela komanso fungo lake. Yesetsani kuganizila mmene anthu ochulidwa m’nkhaniyo ankamvela zinthuzo zikamacitika. Ganizilani zomwe anthuwo anacita ndipo muziyelekeze ndi zimene inuyo mukanacita zikanakhala kuti zinthuzo zacitikila inuyo.” Komabe, sitiyenela kuganizila za m’maganizo mwathu. M’malo mwake, tiyenela kuganizila zimene nkhani youzilidwa imeneyo ikukamba za munthu wochulidwayo. Kucita zimenezi kumafuna nthawi yosinkhasinkha. (Neh. 8:8) Ngati phunzilo likuyambila mkati mwa mutu, wocititsa ayenela kubweleza zimene tinaphunzila mlungu watha kwa masekondi 30 kapena 60. Wocititsa ayenela kufunsa funso limodzi kapena aŵili pothela pa phunzilo ngati lilibe kamutu kakuti “Mfundo Zofunika Kuziganizira . . . ”
4. N’cifukwa ciani tiyenela kuphunzila buku la Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo?
4 Tikukhala m’dziko loipa pamene tsiku ndi tsiku timakumana ndi zinthu zimene zingaononge cikhulupililo cathu. Buku lino komanso nkhani zimene zimatuluka mu Nsanja ya Mlonda, ndi mphatso zocokela kwa Yehova zotithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu.(Yak. 1:17) Conco,tiyeni tikaligwilitsile nchito bwino mwa kupezeka pa Phunzilo la Baibulo la Mpingo nthawi zonse, ndi kuyankhapo mmene tingathele.