Mukhoza Kukhalabe Wodzicepetsa Ngakhale pa Ciyeso
“Uziyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako.”—MIKA 6:8.
1-3. Kodi mneneli wa ku Yuda amene sanam’tomole dzina, analephela kucita ciani? Nanga cinam’citikila n’ciani? (Onani pikica pamwambapa)
PANTHAWI ya ulamulilo wa Mfumu Yerobowamu, Yehova anatuma mneneli wa ku Yuda kukapeleka uthenga waciweluzo kwa mfumu yopandukayo ya Isiraeli. Mneneli wodzicepetsa ndi wokhulupilika ameneyo anapelekadi uthenga wa Mulungu, ndipo Yehova anam’teteza ku mkwiyo wa Yerobowamu.—1 Maf. 13:1-10.
2 Mneneli ameneyo pobwelela kwawo, anakumana ndi mkulu wina wacikalambile wa ku Beteli, mzinda wapafupi. Mkuluyo anakamba kuti anali mneneli wa Yehova. Iye ananyengelela mneneli wa Mulungu wacicepelepoyo ndi kum’pangitsa kutaya malangizo ofunika a Yehova, akuti ‘asakadye cakudya kapena kumwa madzi, ndi akuti ‘asakadzele njila imene adutse popita.’ Zimenezi zinam’kwiyiitsa Yehova. Ali pa ulendo wobwelela kwawo, anangoona nkhalamu balamanthu! n’kum’phelatu pamenepo.—1 Maf. 13:11-24
3 N’cifukwa ciani mneneli amene anali wodzicepetsa poyamba anamvelela wokalamba wacinyengo ameneyo? Baibo siifotokoza. Koma n’kutheka kuti anaiŵalilatu zakuti anafunika kuyenda ‘modzicepetsa ndi Mulungu wake.’ (Ŵelengani Mika 6:8.) M’Baibo, kuyenda na Yehova kumatanthauza kum’dalila, kucilikiza ucifumu wake, na kutsatila citsogozo cake. Munthu wodzicepetsa amazindikila kuti afunika kumakambitsana nthawi zonse ndi Atate wake wacikondi ndi wamphamvu zonse. Mneneliyo akanafunsila kwa Yehova kuti amvetsetse bwino malangizo ake. Koma Malemba satiuza kuti iye anacita zimenezo. Nafenso, nthawi zina zingativute kupanga cosankha cifukwa cosadziŵa bwino-bwino njila yoyenelela. Tikadzicepetsa ndi kupempha citsogozo ca Yehova, tidzapewa kupanga zosankha zimene zingatigwetsele m’mavuto aakulu.
4. Tidzaphunzilanji m’nkhani ino?
4 M’nkhani yapita, tinaphunzila cifukwa cake kudzicepetsa kukali kofunika masiku ano, na mmene tingakuonetsele. Kodi n’zocitika ziti zimene zingatiike paciyeso pa nkhani ya kudzicepetsa? Nanga tingakulitse bwanji khalidwe la kudzicepetsa, limene lingatithandize pa mayeselo? Kuti tipeze mayankho, tiyeni tikambilane zocitika zitatu zimene zingatiike paciyeso pa nkhani ya kudzicepetsa. Tidzaonanso mmene tingacitile mwanzelu pacocitika ciliconse.—Miy. 11:2.
ZINTHU ZIKASINTHA MU UMOYO WATHU
5, 6. Kodi Barizilai anaonetsa bwanji mzimu wodzicepetsa?
5 Kusintha kwa zinthu mu umoyo wathu, kapena mu utumiki wathu, kungakhale ciyeso pa kudzicepetsa kwathu. Pamene Davide anapempha Barizilai wa zaka 80, kuti akakhale ku nyumba ya mfumu, unali mwayi wapadela kwa Barizilai. Anakavomela, sembe anali kusangalala ndi maceza ndi mfumuyo. Koma Barizilai sanavomele. Cifukwa ciani? Pokhala wacikalambile, iye anauza Davide kuti sanafune kukakhala mtolo kwa mfumu. Mwa ici, Barizilai anapeleka mwana wake Chimamu, kuti akakhale kwa mfumu m’malo mwa iye.—2 Sam. 19:31-37.
6 Kudzicepetsa ndiye kunathandiza Barizilai kupanga cosankha canzelu. Cimene anakanila pempho la Davide sicinali kuopa kuti sangakwanitse udindowo ayi, kapena kungofuna kusangalala ndi kupuma kwake panchito ayinso. Barizilai anazindikila kuti zinthu kwa iye zinasintha tsopano, ndipo anali wacikulile. Sanafune kungosanjikiza maudindo. (Ŵelengani Agalatiya 6:4, 5.) Ngati mtima wathu umangokhala pa udindo kapena kuchuka, tidziŵe kuti tikubyala mbewu ya kudzimvela ndi mpikisano, ndipo cophukapo cake cidzakhala kugwilitsidwa mwala koŵaŵa. (Aga. 5:26) Koma kudzicepetsa kumathandiza onse kuika pamodzi maluso awo kuti Mulungu atamandike, ndi kuti athandizane bwino lomwe.—1 Akor. 10:31.
7, 8. Kudzicepetsa kungatithandize bwanji kupewa kudalila nzelu zathu?
7 Udindo waukulu umabwelanso na ulamulilo waukulu. Mpamene munthu amaonekela kuti ni wodzicepetsa kapena ayi. Nehemiya atamva za mavuto a anthu ku Yerusalemu, anacondelela Yehova m’pemphelo. (Neh. 1:4, 11) Dalitso la Yehova linafika pamene Mfumu Aritasasita anasankha Nehemiya kukhala bwanamkubwa wa delalo. Ngakhale kuti anali na udindo wapamwamba, cuma, na ulamulilo waukulu, Nehemiya sanadzidalile yekha kapena kudalila maluso ake. Anapitilizabe kuyenda na Mulungu. Nthawi zonse anali kufunsila mwa kufufuza m’Cilamulo ca Mulungu. (Neh. 8:1, 8, 9) Nehemiya sanali kuyang’anila ena mowapondeleza. Anali kuwatumikila mosewezetsa cuma cake.—Neh. 5:14-19.
8 Citsanzo ca Nehemiya cionetsa mmene kudzicepetsa kungatithandizile kupewa kudalila nzelu zathu pamene utumiki wathu wasintha, kapena udindo. Cifukwa codalila luso lake, mkulu angayambe kumasamalila maudindo a mpingo, monga kukamba nkhani, osayamba wapemphela n’komwe kwa Yehova. Ena angamayambe n’kupanga cosankha, ndiyeno n’kupemphela kuti Yehova adalitse cosankha cawo. Kodi tingati kumeneko n’kudzicepetsa? Munthu wodzicepetsa saiŵala kudalila Yehova ndipo amadziŵa malo ake m’makonzedwe a Mulungu. Maluso athu mwa iwo okha si kanthu. Maka-maka pamene ticita na vuto kapena nkhani imene tinaizoloŵela, tifunika kusamala kuti tisadalile nzelu zathu. (Ŵelengani Miyambo 3:5, 6.) Monga a m’banja la cikhulupililo, timafuna kuthandizana kucita bwino mbali zathu m’banja kapena mumpingo. Sitili na maganizo ongofuna mpando ndi kuchuka, ngati mmene anthu amacitila kunjaku.—1 Tim. 3:15.
MUKATSUTSIDWA KAPENA KUTAMANDIDWA
9, 10. Kodi kudzicepetsa kungatithandize bwanji ena akamatinyoza popanda cifukwa?
9 Anthu akatinyoza popanda zifukwa zingakhale zovuta kupilila. Hana anali kulila nthawi zambili cifukwa comatonzedwa na mkazi mnzake Penina. Ngakhale kuti mwamuna wake anali kum’konda, Hana sanali kubeleka. Tsiku lina, Hana akupemphela pa kacisi, Mkulu wa Ansembe Eli anam’nena kuti waledzela. Taganizani zimenezo! Koma Hana anakhalabe wodziletsa, ndipo anayankhabe mwaulemu kwa Eli. Pemphelo lake lokhudza mtima limapezeka m’Baibo. Ni pemphelo la mau oonetsa cikhulupililo, acitamando, ndi oyamikila.—1 Sam. 1:5-7, 12-16; 2:1-10.
Kodi mavalidwe anthu ndi mmene timadzikonzela, zimaonetsa kuti timalemekeza Yehova na anzathu, kapena ayi? (Onani palagilafu 12)
10 Kudzicepetsa kungatithandize ‘kupitiliza kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino.’ (Aroma 12:21) Zocitika zambili m’dziko lino la Satana n’zopanda cilungamo. Conco tifunika kudziletsa kwambili kuti tisamapse mtima ndi makhalidwe a anthu oipa. (Sal. 37:1) Mikangano imapweteka kwambili ikacitika pakati pa abale ndi alongo. Koma munthu wodzicepetsa amatengela citsanzo ca Yesu. Baibo imati: “Pamene anali kunenedwa zacipongwe, sanabwezele zacipongwe. . . , koma anali kudzipeleka kwa iye amene amaweluza molungama.” (1 Pet. 2:23) Yesu anali kudziŵa kuti kubwezela n’kwa Yehova. (Aroma 12:19) Ifenso Akhiristu tikulangizidwa kukhala odzicepetsa ndi kupewa ‘kubwezela coipa pa coipa.’—1 Pet. 3:8, 9.
11, 12. (a) Kodi kudzicepetsa kungatithandize bwanji ngati ena atiyamikila kapena kutitamanda mopambanitsa? (b) Nanga kungatithandize bwanji pa nkhani ya mavalidwe ndi kudzikonza, ndiponso pa khalidwe lathu?
11 Komanso, kuyamikilidwa kapena kutamandidwa mopambanitsa kungabweletsenso ciyeso pa kudzicepetsa kwathu. Ganizilani mmene Esitere anakhalilabe wodzicepetsa pamene zinthu zinamuyendela bwino kopambana. Ngakhale kuti iye anali wokongola kale mocititsa kaso, anam’samalila ndi kum’konzekeletsa kwa caka conse. Tsiku na tsiku anali kuyanjana ndi atsikana ambili ocokela kumadela onse a ufumu wa Peresiya. Onse anali pa mpikisano wa mbeta kuti mfumu isankhepo mmodzi. Ngakhale n’conco, Esitere anakhalabe waulemu ndi wodzicepetsa. Ngakhale pamene mfumu inamusankha kukhala mfumukazi yake, iye sanadzitukumule kapena kunyadila ena ayi.—Esitere 2:9, 12, 15, 17.
12 Kudzicepetsa kumatithandizanso kuvala mwaulemu, ndi kudzikonza mwacikatikati. Anthu amakopeka nafe cifukwa ca “mzimu wabata ndi wofatsa,” osati kudzitama kapena kudzionetsela iyayi. (Ŵelengani 1 Petulo 3:3, 4; Yer. 9:23, 24) Ngati tisunga maganizo oipa mumtima mwathu, m’kupita kwa nthawi adzaonekela m’kacitidwe kathu ka zinthu. Mwacitsanzo, kakambidwe kathu cabe ngakhale koonetsa mzimu uja wakuti ‘nili na udindo wapadela ine, nimakhalako na mwayi wodziŵa nkhani zina zacinsinsi, kapena kuti nimadziŵana ndi abale amaudindo akulu-akulu ine.’ Mwinanso timakonda kufotokoza zinthu mwa njila yakuti ciyamikilo cibwele kwambili kwa ife kuposa ena pa zimene zakwanilitsidwa, ngakhale kuti enanso anaikapo maganizo awo. Apanso Yesu anapeleka citsanzo cabwino. Yesu nthawi zambili anali kugwila mau a m’Malemba Acihebeli. Anacita zimenezo kuti omvela aone kuti anali kukamba zocokela kwa Yehova, osati za m’nzelu zake iyai.—Yoh. 8:28.
PAMENE SITILI OTSIMIKIZA
13, 14. Kodi kudzicepetsa kungatithandize bwanji kupanga zosankha zabwino?
13 Cinanso cimene cingatiike pa ciyeso pa nkhani ya kudzicepetsa ni popanga zosankha. Pamene mtumwi Paulo anali ku Kaisareya, mmeneli Agabo anam’cenjeza kuti akapita ku Yerusalemu akamangidwa, ngakhale kuphedwa kumene. Poopa zimenezi abale anam’condelela kuti asapite. Koma Paulo sanasinthe maganizo. Sikuti anadzidalila kwambili ayi, komanso sanakhwethemuke cifukwa ca mantha. Anaika cidalilo conse mwa Yehova, ndipo anali wokonzeka kukwanilitsa utumiki wake kulikonse kumene Yehova akanam’tumiza. Abalewo ataona zimenezi, modzicepetsa analola kuti Paulo apite ku Yerusalemu.—Mac. 21:10-14.
14 Kudzicepetsa kungatithandizenso kupanga zosankha zabwino ngakhale pamene sitidziŵa mmene zinthu zidzakhalila. Mwacitsanzo, ngati tifuna kuyamba utumiki wa nthawi zonse, tingadzifunse kuti, N’ciani cidzacitika nikadzadwala? Bwanji ngati makolo anthu okalamba adzafunikila cisamalilo cathu? Nanga ife tikadzakalamba, n’ndani adzatisamalila? Ngakhale tipemphele bwanji, kapena tifufuze bwanji, sitingapeze mayankho otsimikizika pa mafunso a mtundu umenewu. (Mlal. 8:16, 17) Kudalila Yehova kudzatithandiza kuzindikila ndi kuvomeleza, kuti sitingakwanitse kucita zonse zimene tifuna. Tiyenela kufufuza, kufunsilako kwa ena, ndi kupemphela. Kenako, ticite zimene mzimu wa Mulungu ukutitsogolela. (Ŵelengani Mlaliki 11:4-6.) Pamenepo Yehova adzatidalitsa, kapena kutitsogolela pa zolinga zathu.—Miy. 16:3, 9.
KULITSANI KHALIDWE LA KUDZICEPETSA
15. Kodi kuganizila za Yehova kungatithandize bwanji kukhala wodzicepetsa?
15 Popeza kudzicepetsa kuli ndi maubwino ambili, tingacite bwanji kuti khalidwe limeneli lipitilize kukula mwa ife? Tiyeni tione njila zinayi. Yoyamba, ni kuganizila za makhalidwe apamwamba a Yehova ndi ulemelelo wake. (Yes. 8:13) Kumbukilani kuti timafuna kuyenda ndi Mulungu Wamphamvuzonse, osati mngelo kapena munthu ayi. Kuzindikila mfundo imeneyi kudzatilimbikitsa kukhala ‘odzicepetsa pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.’—1 Pet. 5:6.
16. Kuganizila cikondi ca Mulungu kungatilimbikitse bwanji kukhala wodzicepetsa?
16 Njila yaciŵili, kuganizila cikondi ca Yehova kudzatithandiza kukhala odzicepetsa. Mtumwi Paulo analemba kuti Yehova anapatsa mbali za thupi zosalemekezeka kwambili “ulemu woculuka.” (1 Akor. 12:23, 24) Mofananamo, Yehova amasamalila aliyense wa ife, mosayang’ana zofooka. Satiyelekezela ndi anthu ena, ndipo tikalakwitsa saleka kutikonda. Cifukwa amatikonda, timamva kukhala osungika kulikonse kumene tingam’tumikile m’gulu lake.
17. Kodi kuona zabwino mwa ena kudzatithandiza bwanji?
17 Njila yacitatu, ni kutengela citsanzo ca Yehova coyang’ana zabwino mwa ena. Kuyamikila malo athu mu utumiki wathu kwa Yehova kudzatithandiza kucita zimenezi. M’malo mofuna malo apamwamba kapena kufuna kumatenga malo a ena, tizifunsila kwa ena ndi kumvela maganizo awo. (Miy. 13:10) Ena akapatsidwa udindo kapena utumiki watsopano, tiyeni tikondwele nawo. Ndipo tizitamanda Yehova tikaona mmene akudalitsila “gulu lonse la abale [athu] m’dzikoli.”—1 Pet. 5:9.
18. Kodi cikumbumtima cathu tingaciphunzitse bwanji?
18 Njila yacinayi, tingakulitse kudzicepetsa ngati tiseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kuphunzitsa cikumbumtima cathu. Kuphunzila kuona mmene Yehova amaonela zinthu kudzatithandiza kukhala ndi kaonedwe kabwino. Tingacilimbitse bwino cikumbumtima cathu mwa kuphunzila Baibo, kupemphela, ndi kugwilitsila nchito zimene timaphunzila. (1 Tim. 1:5) Tifunikanso kuika ena patsogolo pathu. Tikamacita mbali yathu, Yehova akutilonjeza kuti ‘adzamalizitsa kutiphunzitsa.’ Inde, adzatiphunzitsa khalidwe la kudzicepetsa, ndi makhalidwe enanso aumulungu.—1 Pet. 5:10.
19. N’ciani cidzatithandiza kukhalabe wodzicepetsa kwamuyaya?
19 Mcitidwe wodzikuza umodzi wokha, unataitsa mneneli wosatomolewa dzina uja, moyo wake ndi ciyanjo ca Yehova. Komabe n’zotheka kukhalabe wodzicepetsa pa mayeselo. Taona umboni za zimenezi kwa anthu okhulupilika akale ndi amakono. Pamene tipitiliza kuyenda na Yehova, kudzicepetsa kwathu nakonso kuyenelanso kukulila-kulila. (Miy. 8:13) Kaya tili pa utumiki wanji pali pano, tidziŵe kuti kuyenda ndi Yehova ndiwo mwayi woposa wina uliwonse. Ucengeteni mwayi umenewo, ndipo pitilizani kuyenda ndi Yehova modzicepetsa kwamuyaya.