‘Zimenezo Uziphunzitse kwa Amuna Okhulupilika’
“Zimenezo uziphunzitse kwa anthu [amuna] okhulupilika amene nawonso, adzakhala oyenelela bwino kuphunzitsa ena.”—2 TIM. 2:2.
1, 2. Kodi anthu ambili amaiona bwanji nchito yawo?
ANTHU ambili amadziŵika na nchito imene amaseŵenza. Kwa ena, nchito kapena udindo ni cizindikilo ca ulemelelo wa munthu. Ku maiko ena, pofuna kudziŵa munthu, amakonda kufunsa kuti, “Mumagwila nchito yanji?”
2 Ngakhale m’Baibo, anthu ena amachulidwa ndi nchito zimene anali kugwila. Mwacitsanzo imati “Mateyu wokhometsa msonkho,” “Simoni wina wofufuta zikopa,” ndi “Luka, dokotala wokondedwa.” (Mat. 10:3; Mac. 10:6; Akol. 4:14) Ndipo anthu ena anadziŵika ndi maudindo awo akuuzimu. Timaŵelenga za Mfumu Davide, mneneli Eliya ndi mtumwi Paulo. Amuna amenewa anayamikila kwambili utumiki umene Mulungu anawapatsa. Ngati nafenso tili na utumiki uliwonse, tiyenela kuucengeta bwino.
3. N’cifukwa ciani acikulile afunika kuphunzitsa acinyamata? (Onani pikica pamwambapa.)
3 Ambili timakonda nchito zathu, ndipo tingakonde kupitiliza nazo kwamuyaya. Koma cosapeweka n’cakuti, kuyambila kwa Adamu, m’badwo uliwonse umakalamba ndi kuloŵedwa m’malo ndi wina. (Mlal. 1:4) M’zaka zaposacedwapa, kusintha kumeneku kwakhala cinthu covuta kucilandila kwa Akhiristu ena. Nchito ya anthu a Yehova ikukulila-kulila, ndipo ikuloŵetsamo zambili. Nchito zambili tsopano zimafuna kutsatila njila za sayansi yamakono zimene zimasintha mofulumila. Njila zimenezi zingakhale zovutilapo kwa acikulile ena. (Luka 5:39) Mwina cifukwa sicingakhale cimeneco. Komabe, acinyamata ndiwo ali na mphamvu ndi nyonga kuposa acikulile. (Miy. 20:29) Conco, ni njila yacikondi komanso yothandiza kuti acikulile azikonzekeletsa acinyamata kutenga maudindo aakulu.—Ŵelengani Salimo 71:18.
4. N’cifukwa ciani cimakhala covuta kwa ena kugaŵilako ena maudindo? (Onani kabokosi kakuti “Zifukwa Zimene Ena Safunila Kugaŵila Ena Maudindo.”)
4 Ena ali pa maudindo, zingawavute kugaŵilako acinyamata maudindo. Ena amaopa kuti pothela pake adzaluza udindo umene amaukonda kwambili. Ena amaopa kutaikidwa ulamulilo, poganiza kuti acinyamata sangayendetse bwino zinthu. Enanso angaganize kuti alibe nthawi yophunzitsa munthu wina. Komanso nawonso acinyamata, afunika kukhala oleza mtima ngati sapatsidwa maudindo owonjezeleka.
5. Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani ino?
5 Tiyeni tikambilane nkhani yogaŵila maudindo pa mbali ziŵili. Mbali yoyamba, kodi acikulile angathandize bwanji acinyamata kutenga maudindo aakulu? Ndipo n’cifukwa ciani zimenezi n’zofunikila? (2 Tim. 2:2) Mbali yaciŵili, n’cifukwa ciani acinyamata afunika kukhala aulemu pamene akuthandizila abale acikulile, ndi kuphunzila kwa iwo? Coyamba, tiyeni tione mmene Mfumu Davide anakonzekeletsela mwana wake kutenga udindo wofunika kwambili.
DAVIDE ANAKONZEKELETSA SOLOMO NDI KUM’CILIKIZA
6. Kodi Mfumu Davide inafuna kucita ciani? Nanga Yehova anati ciani?
6 Atakhala wothaŵa-thaŵa kwa zaka zambili, Davide anakhazikika bwino m’nyumba yacifumu. Koma poona kuti panalibe “nyumba,” kapena kuti kacisi wopelekedwa kwa Yehova, iye anafuna kum’mangila. Conco, anauza mneneli Natani kuti: “Ine ndikukhala m’nyumba ya mitengo ya mkungudza, koma likasa la pangano la Yehova likukhala m’cihema cansalu.” Natani anamuuza kuti: “Citani ciliconse cimene cili mumtima mwanu, cifukwa Mulungu woona ali nanu.” Koma Yehova anapeleka malangizo osiyana. Anauza Natani kuuza Davide kuti: “Si iwe amene udzandimangila nyumba yokhalamo.” Ngakhale kuti Yehova analonjeza Davide kuti adzapitiliza kum’dalitsa, anamuuza kuti mwana wake, Solomo, ndiye adzamanga kacisi. Kodi Davide anacita bwanji?—1 Mbiri 17:1-4, 8, 11, 12; 29:1.
7. Kodi Davide anacitanji atamva zimene Yehova anakamba?
7 Kodi Davide analeka kucilikiza nchitoyo, cifukwa cokwinyilila kuti citamando comanga kacisi sicidzabwela kwa iye? Iyai. N’zoona kuti cimangoco cinachedwa kuti kacisi wa Solomo, osati wa Davide. Ngakhale kuti mwina Davide anakhumudwa kuti sanakwanilitse cokhumba mtima wake, anacilikiza nchitoyo na mtima wonse. Iye analinganiza magulu a anchito, simbi, mkuwa, siliva, golide mitengo. Kuonjezela apo, analimbikitsa Solomo kuti: “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe, ndipo zinthu zikuyendele bwino kuti umange nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga mmene iye analankhulila za iwe.”—1 Mbiri 22:11, 14-16.
8. N’cifukwa ciani mwina Davide anaona ngati Solomo anali wosayenelela? Komabe anacita ciani?
8 Ŵelengani 1 Mbiri 22:5. N’kutheka kuti m’maso mwa Davide, Solomo anam’cepela kuti angayang’anile nchito yofunika kwambili imeneyo. Ndi iko komwe, kacisiyo anali “waulemelelo wosaneneka,” ndipo panthawiyo Solomo anali “wamng’ono komanso wosakhwima.” Koma kumbali ina, Davide anadziŵa kuti Yehova adzam’konzekeletsa Solomo kuti ayendetse bwino nchitoyo. Conco, Davide anaika mtima wake pa kuthandiza Solomo. Anam’thandiza kupeza zomangila zonse zofunikila.
KONDWELANI NDI KUPHUNZITSA ENA
N’zokondweletsa kuona acinyamata akutenga maudindo aakulu (Onani palagilafu 9)
9. Kodi abale acikulile afunika kuiona bwanji nkhani yosiyila acinyamata maudindo? Pelekani citsanzo.
9 Abale acikulile safunika kukwinyilila kukakhala kofunikila kuti asiyile maudindo abale acinyamata. Nchito imapita patsogolo ngati tiphunzitsa acinyamata kuti akatenge maudindo. Amuna apaudindo afunika kukondwela pamene acinyamata amene iwo anawaphunzitsa bwino atenga maudindo. Tiyelekezele conco: Ganizilani tate amene akuphunzitsa mwana wake kuyendetsa motoka. Pamene mwana ali wamng’ono, amangoyang’ana atate wake akuyendetsa. Akasinkhukilapo, atate wake amayamba kum’fotokozela zina ndi zina. Koma akafika pa zaka zovomelezeka ndi boma, amayamba kuyendetsa motokayo pamene atate wake akum’patsa malangizo a moyendetsela. Nthawi zina, akhoza kumasinthana kuyendetsa, ndipo m’kupita kwa nthawi, tateyo amasiyila mwana wake kumayendetsa nthawi zambili. Ndipo akakalamba, kuyendetsa konse amasiyila mwana wake. Atate wanzelu amakondwela kusiya motokayo m’manja mwa mwana wake, ndipo safunika kumamulamulilabe. N’cimodzi-modzinso inu amuna acikulile. Khalani onyadila kuti mwawaphunzitsa nchito acinyamata, ndipo aloleni lomba kuti atenge maudindowo.
10. Kodi Mose anali kuiona bwanji nkhani ya ulemelelo ndi udindo?
10 Abale acikulile, pewani nsanje yakaduka. Kumbukilani mmene Mose anayankhila pamene amuna ena mu msasa wa Aisiraeli anayamba kucita zinthu monga aneneli. (Ŵelengani Numeri 11:24-29.) Yoswa, mthandizi wa Mose, anafuna kuwaletsa. Ayenela anaganiza kuti anthu amenewo anali kusokoneza udindo wa Mose ndi ulamulilo wake. Koma Mose anamuyankha kuti: “Kodi ukucita nsanje cifukwa condidela nkhawa? Ayi usatelo. Ndikanakonda anthu onse a Yehova akanakhala aneneli, cifukwa Yehova akanaika mzimu wake pa iwo!” Mose anaona dzanja la Yehova pa nkhaniyo. M’malo mofunapo ulemelelo wake, Mose anaonetsa kuti akanakonda mphatso zauzimu zimenezo zikanapatsidwanso kwa atumiki onse a Yehova. Mofanana ndi Mose, na ise tizikondwela ena akalandila udindo umene ifenso tikanakonda kuulandila?
11. Kodi m’bale wina anati ciani za kusiyila ena maudindo?
11 Lelo lino, pali abale ambili amene akangalika pamaudindo kwa zaka zambili, ndipo akonzekeletsa acinyamata kutenga maudindowo. Mwacitsanzo, m’bale Peter, atumikila kwa zaka zoposa 74 mu utumiki wa nthawi zonse. Kwa zaka 35 anatumikila pa nthambi ku Europe. Kwazaka zambili anali woyanganila Service Department. Posacedwapa, m’bale Paul, wacinyamata, ni amene anatenga malo ake. Iye anaseŵenza ndi m’bale Paul kwa zaka zambili. M’bale Peter atafunsidwa kuti anamva bwanji na masinthidwe amenewo, anayankha kuti: “Ndine wokondwa ndi wonyadila kuti pali abale amene anaphunzitsidwa kutenga maudindo aakulu, amenenso akuwasamalila bwino ngako.”
TIZIYAMIKILA ACIKULILE PAKATI PATHU
12. Tiphunzilapo ciani pa nkhani ya m’Baibo ya Rehobowamu.
12 Solomo atamwalila, mwana wake Rehobowamu anakhala mfumu. Pamene anafuna uphungu wa mmene angayendetsele ufumu wake, coyamba anakafunsila kwa acikulile. Koma iye anaukana uphungu wawo. M’malomwake, anamvela uphungu wocokela kwa anyamata anzake amene anakula nawo, amenenso panthawiyo anali atumiki ake. Zotulukapo zake zinali masoka okha-okha. (2 Mbiri 10:6-11, 19) Phunzilo? N’cinthu canzelu kufunsila na kumvela uphungu wa acikulile, aciyambakale. Sititanthauza kuti acinyamata azingoyendela njila zakale ayi. Koma asamafulumile kukana uphungu wa acikulile.
13. Ndi motani mmene acinyamata angacitile zinthu mogwilizana ndi acikulile?
13 Pali abale acinyamata amene amayang’anila nchito zimene zimaphatikizapo acikulile. Ngakhale kuti acinyamatawo tsopano ali pamaudindo aakulu, afunika kupitilizabe kufunsila ndi kutapako nzelu kwa aciyambakale pofuna kupanga zosankha. M’bale Paul amene tachula uja, amene anatenga udindo wa m’bale Peter woyang’anila dipatimenti pa Beteli, anati: “N’nali kufunsila uphungu kwa m’bale Peter, ndipo n’nalimbikitsanso ena mu dipatimenti yathu kuti azicita cimodzi-modzi.”
14. Kodi mgwilizano wa Timoteyo na mtumwi Paulo utiphunzitsanji?
14 Wacinyamata Timoteyo anaseŵenza pamodzi na mtumwi Paulo kwa zaka zambili. (Ŵelengani Afilipi 2:20-22.) Paulo analembela abale a ku Korinto kuti: “Ndikukutumizilani Timoteyo, popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupilika mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimacitila zinthu potumikila Khiristu Yesu, monga mmenenso ineyo ndikuphunzitsila kulikonse, mumpingo uliwonse.” (1 Akor. 4:17) Mau acidule amenewa aonetsa kuti panali mgwilizano wamphamvu pakati pa Paulo na Timoteyo. Paulo anacita khama kuphunzitsa Timoteyo ‘mmene amacitila zinthu potumikila Khiristu.’ Nayenso Timoteyo anali munthu wophunzitsika, n’cifukwa cake Paulo anam’konda. N’citsanzo cabwino cotani nanga kwa akulu, pamene aphunzitsa ena kutenga maudindo aakulu mu mpingo.
TONSE TILIPO NA MBALI
15. Tikakhudzidwa na kusintha, kodi uphungu wa Paulo kwa Akhiristu a ku Roma ungatithandize bwanji?
15 Tikukhala m’nthawi yapadela. Gawo la padziko lapansi la gulu la Yehova likukula m’mbali zosiyana-siyana. Koma kukula kumeneku kumaitananso masinthidwe. Pamene masinthidwe atikhudza mwacindunji, tiyeni tikhale odzicepetsa. Tiyang’ane pa cifunilo ca Yehova, osati pa cifunilo cathu. Kucita izi kumalimbikitsa mgwilizano. Polembela Akhiristu ku Roma, Paulo anati: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza m’njila yakuti akhale munthu woganiza bwino, malinga ndi cikhulupililo cimene Mulungu wamupatsa. Pakuti monga tilili ndi ziwalo zambili m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwila nchito yofanana, momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambili, tili thupi limodzi mwa Khiristu.”—Aroma 12:3-5.
16. Kodi acikulile, acinyamata, ndi akazi awo, angacite ciani kuti asungitse mtendele ndi mgwilizano m’gulu la Yehova?
16 Mulimonse mmene zinthu zingakhalile kwa ife, tiyeni tiike patsogolo zinthu za Ufumu wa Yehova. Inu abale acikulile, phunzitsani acinyamata kucita zimene mumacita. Inunso acinyamata, landilani maudindo, khalani odzicepetsa ndipo pitilizani kulemekeza acikulile. Komanso inu akazi a amuna apaudindo, tengelani citsanzo ca Purisikila, mkazi wa Akula. Iye anacilikiza Akula mokhulupilika ngakhale pamene zinthu zinasintha.—Mac. 18:2.
17. Kodi Yesu anali na cidalilo cotani mwa ophunzila ake? Ndipo anawaphunzitsa ciani?
17 Yesu ndiye citsanzo cabwino koposa pankhani yophunzitsa ena kutenga maudindo aakulu. Iye anadziŵa kuti nthawi yake yotumikila idzatha, ndipo ena adzafunika kupitiliza ndi nchitoyo. Ngakhale kuti ophunzila ake anali opanda ungwilo, iye anawadalila, ndipo anawauza kuti adzacita nchito zazikulu kuposa iye. (Yoh. 14:12) Mwa ici, anawaphunzitsa mokwanila, cakuti analalikila uthenga wabwino m’dziko lonse lodziŵika panthawiyo.—Akol. 1:23.
18. Kodi tiyembekezela zotani m’tsogolo? Nanga pali pano tifunika kucita ciani?
18 Pambuyo pa imfa yake, Yesu anaukitsidwa na kupita kumwamba. Kumeneko anakapatsidwa nchito yowonjezeleka. “Anamuika pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamulilo uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse.” (Aef. 1:19-21) Ngati tingamwalile tili okhulupilika Aramagedo isanacitike, tidzaukitsidwa m’dziko latsopano lolungama. Mmenemo tidzakhala ndi nchito zambili zokondweletsa. Koma ngakhale pali pano, pali nchito yofunika ngako, yolalikila uthenga wabwino ndi kupanga ophunzila. Ife tonse, acinyamata ndi acikulile, tikhale na “zocita zambili nthawi zonse mu nchito ya Ambuye.”—1 Akor. 15:58.