Kodi Mudziŵa?
Kodi moto unali “kunyamuliwa” bwanji m’nthawi zakale?
NKHANI ya m’Baibo ya pa Genesis 22:6 imakamba kuti, pokonzekela ulendo wokapeleka nsembe ku malo akutali, Abulahamu “anatenga nkhuni zokawochela nsembe zija n’kumusenzetsa Isaki mwana wake. Iye ananyamula moto ndi mpeni wophela nyama, ndipo iwo anapitila limodzi.”
Malemba safotokoza njila imene anthu anali kuyatsila moto m’nthawi zakale. Pa funso imene tikukambilana, katswili wina anati n’zokaikitsa ngati Isaki ndi Abulahamu ananyamula “lawi la moto ndi kulisunga loyakabe paulendo wawo wonse.” Conco, zioneka kuti cimene anthu anali kunyamula kweni-kweni ni zoyatsila moto.
Komabe, ena amakamba kuti kuyatsa moto kunali kovuta m’nthawi zakale. Mwa ici, anthu anali kukonda kupala moto kwa aneba awo m’malo moyatsa okha. Akatswili ena amakhulupilila kuti Abulahamu ananyamula mtsuko kapena poto wonyamula ndi cheni. M’potomo munali malasha oyaka moto kapena makala amene anapalidwa pamoto wocezela usiku. (Yes. 30:14) Makala onyamulidwa mwa njila imeneyi anali kuwayatsila moto poseŵenzetsa tunthyonthyo nthawi iliyonse paulendo wautali.