CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 10-11
Fanizo la Msamariya Wacifundo
Yesu anapeleka fanizo ili pofuna kuyankha funso lakuti, “Mnzanga amene ndikuyenela kumukonda ndani kwenikweni?” (Luka 10:25-29) Iye anadziŵa kuti m’kupita kwa nthawi, mpingo wacikhristu udzakhala na anthu “osiyana-siyana”—Asamariya, na anthu amitundu ina. (Yoh. 12:32) Fanizo limeneli linaphunzitsa otsatila ake kuti afunika kuyesetsa kukonda anthu, ngakhale amene aoneka kuti ni osiyana nawo kwambili.
DZIFUNSENI KUTI:
Kodi nimawaona bwanji abale na alongo a mitundu ina?
Kodi nimakonda ngako kuceza na anthu amene nimafanana nawo?
Kodi ningafutukule mtima wanga mwa kudziŵana bwino na Akhristu anzanga a mitundu ina? (2 Akor. 6:13)
Nifuna nikapemphe kuti . . .
nikapite naye mu ulaliki
akabwele ku nyumba kwathu ku cakudya
tikacitile pamodzi Kulambila kwa Pabanja kotsatila