CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 17-18
Muzionetsa Kuyamikila
Kodi cocitika ici citiphunzitsa ciani pa nkhani ya kuyamikila?
Ciyamikilo cathu sicifunika cabe kuthela mu mtima koma tifunika kuciwonetsa
Kukamba mau oyamikila mocokela pansi pa mtima kumaonetsa kuti tili na cikondi cacikhristu, ndipo ni cizindikilo cakuti tili na aulemu
Amene amafuna kukondweletsa Khristu ali na udindo kwa anthu onse, wowaonetsa cikondi na kuwayamikila, mosasamala kanthu za dziko lawo, mtundu wawo kapena cipembedzo cawo.