CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 110–118
“Yehova Ndidzamubwezela Ciani?”
Wamasalimo anayamikila kwambili Yehova cifukwa anamupulumutsa ku “zingwe za imfa.” (Sal. 116:3) Iye anali wofunitsitsa kuonetsa kuti amayamikila Yehova mwa kusunga malonjezo ake onse ndi kum’tumikila modzipeleka.
N’zinthu ziti zimene Yehova wanicitila mlungu uno kuti nimuyamikile?
Ningaonetse bwanji kuti namuyamikila Yehova?