UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kuteteza Mgwilizano Wathu Wapadela
CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Usiku wakuti maŵa Yesu aphedwa, anapemphela kuti ophunzila ake “akhale mu umodzi weni-weni.” (Yoh. 17:23) Kuti tikhale ogwilizana, tifunika kuonetsana cikondi cimene “sicisunga zifukwa.”—1 Akor. 13:5.
MMENE TINGACITILE:
Tengelani citsanzo ca Yehova mwa kuyang’ana zabwino mwa ena
Muzikhululukila ena na mtima wonse
Mukakambilana ndipo nkhaniyo yatha, osaiutsanso.—Miy. 17:9
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—MUSAMASUNGE ZIFUKWA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
M’mbali yoyamba ya vidiyo, kodi Helen anaonetsa bwanji kuti anali ‘kusunga zifukwa’?
M’mbali yaciŵili ya vidiyo, kodi Helen anacita ciani kuti agonjetse maganizo oipa na kukhala na maganizo oyenela?
Kodi Helen anathandizila bwanji kuti mpingo ukhale wogwilizana?
N’ndani amene amavulazika kwambili ngati tisunga zifukwa?