CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 4-5
Anapitiliza Kulankhula Mawu a Mulungu Molimba Mtima
4:5-13, 18-20, 23-31
N’ciani cinathandiza atumwi kukhala aphunzitsi oyenelela? N’ciani cinawathandiza kukamba mwa cidalilo komanso molimba mtima? Iwo “anali kuyenda ndi Yesu,” Mphunzitsi Waluso, ndipo anaphuzila kwa iye. (Mac. 4:13) Kodi tingaphunzile zotani kwa Yesu zimene zingatithandize kukhala aphunzitsi a Baibo aluso?