CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 27-28
Paulo Apita ku Roma
27:23, 24; 28:1, 2, 16, 17
Paulo sanaleke kulalikila ena ngakhale kuti anali mkaidi. Pamene iye anali m’ngalawa, analalikila anthu oyendetsa ngalawayo komanso amene anali naye paulendowo. Ngalawa itasweka pa cilumba ca Melita, mosakayikila iye anatengelapo mwayi wolalikila anthu amene anawacilitsa. Pambuyo pa masiku atatu Paulo atafika ku Roma, anaitana amuna olemekezeka pakati pa Ayuda kuti awalalikile. Pa zaka ziŵili zimene iye anali pa ukaidi wa pa nyumba, analalikila onse obwela kudzamuona.
Mungacite ciani kuti muzilalikila uthenga wabwino olo kuti muli na zopinga?