UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mmene Tonse Tingatengeleko Mbali pa Kusamalila Malo Athu Olambilila
Nyumba zathu za Ufumu si nyumba wamba. Ni malo olambilila opatulidwa kwa Yehova. Kodi aliyense wa ise angacite ciani kuti azitengako mbali posamalila Nyumba ya Ufumu?
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI KUSAMALILA MALO ATHU OLAMBILILA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
N’cifukwa ciani timakhala na malo osonkhanamo?
N’cifukwa ciani tiyenela kusunga Nyumba yathu ya Ufumu ili yoyela komanso yokonzedwa bwino?
Kodi mwapindula bwanji potengako mbali m’pulogilamu yoyeletsa na kukonza zinthu?
N’cifukwa ciani kupewa ngozi n’kofunika? Nanga mu vidiyoyi mwaonamo zitsanzo zanji zopewela ngozi?
Kodi tingalemekeze bwanji Yehova mwa zopeleka zathu?
N’DZAYAMBA KUTHANDIZILA POCITA IZI.