CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 1 ATESALONIKA 1-5
“Pitilizani Kutonthozana ndi Kulimbikitsana”
5:11-14
Mkhristu aliyense, angakwanitse kulimbikitsa ena. Mwacitsanzo, timalimbikitsa Akhristu anzathu ngati tipezeka pa misonkhano nthawi zonse, komanso ngati tigwila nawo nchito yolalikila. Mwina timacita zimenezi “movutikila kwambili,” cifukwa ca thanzi lofooka kapena zovuta zina. (1 Ates. 2:2) Kuwonjezela apo, tingakonzekeletu kapena kufufuzilatu kukali nthawi, zinthu zolimbikitsa zimene tingakambe kwa wokhulupilila mnzathu amene afunika cilimbikitso.
N’kuti kumene mungapeze mfundo zolimbikitsila munthu amene wakumana na vuto linalake?
N’ndani amene mungakonde kumulimbikitsa mu mpingo?