UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Nchito Zabwino Zimene Sizidzaiŵalidwa
Atumiki onse a Yehova angathe kugwila nchito yopatulika imene iye adzawakumbukila nayo mpaka kale-kale. Monga kholo lacikondi limene limanyadila zimene mwana wake wakwanitsa kucita, Yehova saiŵala nchito yathu na cikondi cimene timaonetsa pa dzina lake. (Mat. 6:20; Aheb. 6:10) N’zoona kuti maluso na zocitika mu umoyo zimasiyana-siyana. Koma ngati ticita zonse zimene tingathe potumikila Yehova, tidzakhala acimwemwe. (Agal. 6:4; Akol. 3:23) Kwa zaka zambili, abale na alongo masauzande akhala akutumikila pa Beteli. Kodi mungadzipeleke kuti mukatumikileko pa Beteli? Ngati simungatelo, bwanji osalimbikitsako wina wake kuti akaciteko utumikiwu, kapena kuthandiza wa m’Banja la Beteli kuti apitilize kutumikila m’njila yapadela imeneyi?
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI DZIPELEKENI KUKACITA UTUMIKI WA PA BETELI, PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AYA:
N’ciani ciyenela kulimbikitsa munthu kucita utumiki wa pa Beteli?
Kodi abale na alongo ena akamba zotani zokhudza madalitso amene apeza cifukwa cotumikila pa Beteli?
Kodi pali ziyenelezo zotani za utumiki wa pa Beteli?
Mungafunsile motani utumiki wa pa Beteli?