UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Pitilizani Kuganizila Zimenezi”
Zotani? Afilipi 4:8 ikamba kuti tifunika kuganizila zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambili, zilizonse zolungama, zilizonse zoyela, zilizonse zacikondi, zilizonse zoyamikilika, khalidwe labwino lililonse, ndi ciliconse cotamandika. Koma izi sizitanthauza kuti Akhristu afunika kumangoganizila za Baibo nthawi zonse. Ngakhale n’conco, zimene timasinkha-sinkha ziyenela kukhala zokondweletsa Yehova. Siziyenela kukhala zimene zingatilepheletse kukhala wokhulupilika kwa iye.—Sal. 19:14.
Kupewa maganizo oipa kumakhala kovuta. Timafunika kulimbana na matupi athu opanda ungwilo komanso Satana, “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4) Popeza kuti mphamvu yake imagwila nchito pa zocitika za pa TV, mawailesi, intaneti, ndiponso m’mabuku, zinthu zikuipila-ipila. Ngati sitisankha bwino zinthu zimene tiloŵetsa m’maganizo mwathu, maganizo athu angaipitsidwe, ndipo m’kupita kwa nthawi khalidwe lathu lingasinthe.—Yak. 1:14, 15.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MUZIPEWA ZINTHU ZIMENE ZINGAKULEPHELETSENI KUKHALA WOKHULUPILIKA—ZOSANGULUTSA ZOIPA, PAMBUYO PAKE KAMBILANANI MAFUNSO AYA:
Kodi m’bale anali kutamba ciani pa foni yake? Nanga zinam’khudza bwanji?
Kodi malemba aya, Agalatiya 6:7, 8, ndiponso Salimo 119:37 anamuthandiza bwanji?