UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kugwilizana Pakati pa Kusunga Umphumphu na Maganizo Athu
Timaonetsa kuti tili na mtima wosagaŵikana osati mwa zokamba na zocita zathu cabe, koma mwa zimenenso timaganiza. (Sal. 19:14) Cotelo, Baibo imatilimbikitsa kuti tiziganizila zinthu zilizonse zoona, zofunika, zolungama, zoyela, zacikondi, zolemekezeka, khalidwe labwino lililonse, komanso zotamandika. (Afil. 4:8) N’zoona kuti sitingaletseletu maganizo olakwika kuloŵa mu mtima mwathu. Komabe, kudziletsa kungatithandize kucotsa maganizo oipa na kuyamba kuganizila zabwino. Tikakhala osagaŵikana m’maganizo mwathu, zidzatithandiza kukhalanso osagaŵikana m’zocita zathu.—Maliko 7: 21-23.
Pansi pa lemba lililonse, lembani kaganizidwe komwe tiyenela kupewa:
Afil. 3:13