UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Yehova Amakonda Anthu Aukhondo
“Uzisamba m’manja. Uziyeletsa cipinda cako. Uzipyanga m’mnyumba. Uzitaya vinyalala.” Mwa kukamba mawu amenewa, makolo ambili amaphunzitsa ana awo mmene angakhalile aukhondo. Koma mfundo za kukhala aukhondo zimacokela kwa Mulungu wathu woyela. (Eks. 30:18-20; Deut. 23:14; 2 Akor. 7:1) Ngati timasunga thupi lathu na zinthu zathu mwaukhondo, timalemekeza Yehova. (1 Pet. 1:14-16) Nanga bwanji ponena za nyumba zathu na malo okhala? Mosiyana na anthu amene amataya vinyalala citaye-taye m’njila na m’mapaki, Akhristu amayesetsa kusunga dziko lapansi mwaukhondo. (Sal. 115:16; Chiv. 11:18) Ngakhale kutaya tunthu tung’ono-tung’ono monga tumapepa twa maswiti, mabotolo ya dilinki, kapena mababugamu, kungaonetse mmene timaonela nkhani ya ukhondo. M’mbali zonse za umoyo wathu, tifunika kuonetsa kuti “ndife atumiki a Mulungu.”—2 Akor. 6:3, 4.
TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI, MULUNGU AMAKONDA ANTHU OYELA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:
Kodi anthu ena amakamba kuti n’ciani cimawalepheletsa kusunga zinthu zawo mwaukhondo?
Kodi Cilamulo ca Mose cinaonetsa bwanji maganizo a Yehova pa nkhani ya ukhondo?
Kodi tingacitile bwanji umboni za Yehova popanda kukamba ciliconse?
Kodi ningaonetse bwanji kuti nimatengela maganizo a Yehova pa nkhani ya ukhondo mu umoyo wanga?