LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb19 November tsa. 8
  • Yehova Adziŵa zimene Tifunikila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Adziŵa zimene Tifunikila
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Nkhani Zofanana
  • Misonkhano Ikulu-ikulu Yapacaka Imatipatsa Mwayi Woonetsana Cikondi
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Misonkhano Yolimbikitsa ‘Cikondi na Nchito Zabwino’
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Kusonkhana Pamodzi Kuti Tilambile Mulungu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Kodi Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu Ndani?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
mwb19 November tsa. 8
Alongo akuomba m’manja pa msonkhano wacigawo

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova Adziŵa Zimene Tifunikila

Kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amatipatsa cakudya “pa nthawi yoyenela,” kuonetsa kuti Yehova, amene akutsogolela kapoloyo, adziŵa zimene timafunikila mwauzimu. (Mat. 24:45) Cakudya ca pa nthawi yoyenela ciphatikizapo misonkhano yacigawo na misonkhano ya mkati mwa wiki.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI LIPOTI YA 2017 YA KOMITI YOYANG’ANILA NCHITO YOPHUNZITSA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Anthu ocita msonkhano wacigawo adzala m’sitediyamu

    N’ndani amene ayenela kulandila citamando kaamba ka misonkhano yacigawo ya pa nthawi yake imene timakhala nayo? Cifukwa ciani?

  • Kodi nchito yokonzekela msonkhano wacigawo imayamba liti?

  • A mu Audio/Video Services akunjambula vidiyo ya msonkhano wacigawo

    Kodi amasankha bwanji mitu na nkhani za misonkhano yacigawo?

  • Kodi pamakhala nchito zotani pokonzekela misonkhano yacigawo?

  • Kodi njila zophunzilila za m’sukulu ya Giliyadi amaziseŵenzetsa bwanji pokonza nkhani zophunzila pa misonkhano ya mkati mwa wiki?

  • M’bale ali na kabuku ka umoyo ka misonkhano ya mkati mwa wiki

    Kodi madipatimenti osiyana-siyana amaseŵenzela bwanji pamodzi pokonza kabuku ka misonkhano?

Kodi mumamvela bwanji cifukwa ca zinthu zauzimu zimene Yehova amatipatsa?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani