CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 7-9
Khamu Lalikulu Losaŵelengeka Likudalitsidwa na Yehova
7:9, 14-17
N’cifukwa ciani Yehova akudalitsa khamu lalikulu?
Iwo “akuimilila pamaso pa mpando wacifumu” wa Yehova, mwa kucilikiza ndi mtima wonse ucifumu wake
Iwo avala “mikanjo yoyela,” kuonetsa kuti ni oyela, ndiponso kuti akuimilila pamaso pa Yehova mwacilungamo cifukwa ca cikhulupililo cawo mu nsembe ya Khristu
Iwo akucita “utumiki wopatulika usana ndi usiku,” mwa kulambila Yehova mosalekeza ndiponso mwakhama
Ningacite ciani kuti nikhale mmodzi wa khamu lalikulu?