CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 23-24
Usatsatile Khamu la Anthu
23:1-3
Yehova anacenjeza mboni na oweluza kuti pa milandu asamasonkhezeledwe na khamu la anthu kuti apeleke umboni wabodza kapena kuweluza mopanda cilungamo. Mfundo imeneyi ya kusatsatila khamu la anthu igwilanso nchito m’mbali zina za umoyo wathu. Nthawi zonse dzikoli limalimbikitsa Akhristu kuti aziganiza na kucita zinthu m’njila imene anthu osalemekeza Yehova amacitila.—Aroma 12:2.
N’cifukwa ciani si canzelu kutsatila khamu la anthu pamene
tamvela nkhani zopanda umboni kapena mijedo?
tisankha zovala, makonzedwe a tsitsi, komanso zosangalatsa?
tiganizila na kucita zinthu ndi anthu osiyana nawo mtundu, cikhalidwe, kapena zacuma?