CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 15-17
“Yehova Anasintha Dzina la Abulamu na Sarai—Cifukwa?”
17:1, 3-5, 15, 16
Yehova anaona Abulamu kukhala wopanda colakwa pamaso pake. Atafotokoza zowonjezeleka zokhudza lonjezo lake kwa Abulamu, Mulungu anapatsa Abulamu na Sarai maina okhala na matanthauzo a ulosi.
Mogwilizana na maina awo, Abulahamu anakhala Tate wa mitundu yambili, ndipo Sara anakhala kholo la mafumu.
Abulahamu
Tate wa Khamu
Sara
Mfumukazi
Pobadwa, sitidzisankhila tekha dzina limene tidzapatsidwa. Koma mofanana na Abulahamu na Sara, tingadzipangile tekha dzina labwino. Dzifunseni kuti:
‘Kodi ningacite ciani kuti Yehova aziniona kukhala wopanda colakwa?’
Kodi nikupanga dzina lotani kwa Yehova?