CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 24
Mkazi wa Isaki
24:2-4, 11-15, 58, 67
Mtumiki wa Abulahamu anapempha Yehova kuti amuthandize kusankha mkazi wa Isaki. (Gen. 24:42-44) Na ife tifunika kupempha citsogozo ca Yehova tisanapange zosankha zikulu-zikulu. Motani?
Pemphelani
Fufuzani m’Mawu a Mulungu na m’zofalitsa zathu
Pemphani thandizo kwa Akhristu ofikapo kuuzimu