LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 March tsa. 7
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Akhungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Akhungu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Thandizani Anthu Akhungu Kuphunzila za Yehova
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Zidindo Zimene Zimasintha Miyoyo ya Anthu
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
  • Anaona Cikondi Ceniceni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 March tsa. 7
Mlongo wakhungu akuseŵenzetsa manja ake poŵelenga cofalitsa ca anthu akhungu.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu Mu Ulaliki​—Kulalikila Anthu Akhungu

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Anthu ambili akhungu sakhala omasuka kukamba na ŵanthu osaŵadziŵa. Conco pamafunika luso kuti tilalikile anthu amenewa. Yehova amawakonda anthu akhungu. (Lev. 19:14) Tingatengele citsanzo cake mwa kucitapo kanthu kuti tiwathandize mwauzimu.

MMENE TINGACITILE:

  • “Fufuzani” anthu akhungu. (Mat. 10:11) Kodi mudziŵako munthu amene wacibale wake ni wakhungu? Kodi m’gawo lanu muliko masukulu, nyumba zosungilamo anthu osaona amene angafuneko zofalitsa za anthu akhungu?

  • Onetsani mzimu waubwenzi. Kukhala waubwenzi komanso kuonetsa cidwi ceni-ceni kungathandize munthu wakhungu kukhala womasuka. Yesani kuyambitsa makambilano pa nkhani zimene anthu akhungu angacite nazo cidwi

  • Pelekani thandizo la kuuzimu. Pofuna kuthandiza anthu akhungu, gulu lathu lakonza zofalitsa m’mipangidwe yosiyana-siyana. Mungafunse wakhungu kuti afotokoze njila yophunzilila imene afuna. Woyang’anila utumiki afunika kuonetsetsa kuti mtumiki wa mabuku waitanitsa mabuku a anthu akhungu mu mpangidwe umene munthu wakhungu aliyense afuna.

Zofalitsa za anthu osaona bwino komanso akhungu zilipo m’vitundu vingapo m’mipangidwe iyi:

  • Zomvetsela za pa JW Laibulale na za pa webusaiti yathu

  • Malembo aakulu

  • Mabuku a anthu akhungu

  • Mafaelo oseŵenzetsa pacipangizo ca notetaker

  • Mafaelo oseŵenzetsa pa screen reader (mapulogilamu a pa kompyuta amene amaŵelenga mokweza zilizonse zimene zili pa sikilini)

Zithunzi: 1. Mlongo akuŵelenga cofalitsa ca anthu akhungu. 2. Mlongo akuseŵenzetsa cipangizo ca notetaker.

Akuŵelenga buku la anthu akhungu ndiponso akulemba manotsi pa cipangizo colembela ca akhungu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani