LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 5/15 masa. 2-3
  • Thandizani Anthu Akhungu Kuphunzila za Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Thandizani Anthu Akhungu Kuphunzila za Yehova
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Zofanana
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Anthu Akhungu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Zidindo Zimene Zimasintha Miyoyo ya Anthu
    Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 5/15 masa. 2-3

Thandizani Anthu Akhungu Kuphunzila za Yehova

1. Kodi Yesu anaonetsa bwanji cifundo kwa anthu akhungu?

1 Panali patatsala masiku ocepa kuti Yesu aphedwe. Pamene anali kutuluka mu mzinda wa Yeriko, amuna aŵili akhungu opemphapempha anafuula kwa iye kuti: “Ambuye, ticitileni cifundo!” Ngakhale kuti Yesu anali kuganizila mavuto aakulu amene anali kudzamucitikila, iye anaima ndi kuwaitana kuti abwele kwa iye, ndipo anaŵacilitsa. (Mat. 20:29-34) Kodi tingatengele bwanji khalidwe lacifundo limene Yesu anaonetsa kwa anthu akhungu?

2. (a) Kodi tingamulalikile bwanji munthu wakhungu amene takumana naye?

2 Athandizeni: Mukakumana ndi munthu wakhungu, mwina pagulu, zidziŵikitseni ndipo muuzeni kuti ndinu wokonzeka kumuthandiza. Popeza kuti anthu amenewa nthawi zambili amawacitila zinthu zacipongwe, poyamba io angacite mantha. Koma ngati mucita zinthu mwaubwenzi ndi kuwaonetsa cidwi, io angamasuke nanu. Dziŵani kuti anthu amafa maso pamlingo wosiyanasiyana, ndipo zimenezi zingaonetse thandizo limene mungapeleke. Conco pambuyo pothandiza munthu wakhungu, mwina mungamuuze kuti mukugwila nchito yophunzitsa Baibulo. Ndiyeno muŵelengeleni Salimo 146:8 kapena Yesaya 35:5, 6. Ngati amakwanitsa kuŵelenga zilembo za anthu akhungu, mufunseni ngati angakonde kukhala ndi cofalitsa ca zilembo za akhungu cimene cingamuthandize kudziŵa zambili za m’Baibulo. Mungamuthandizenso kutenga nkhani zomvetsela cabe pa jw.org. Ngati kompyuta yake ili ndi pulogalamu yosintha mau olembedwa amene ali mukompyutayo n’kukhala omvetsela, mungamutengele nkhani pa jw.org limodzi ndi zofalitsa zina za zilembo za anthu akhungu za RTF (Rich Text Format).—Onani bokosi la mutu wakuti, “Zimene Mungacite Pothandiza Munthu Wakhungu. . .”

3. Tingafufuze bwanji anthu akhungu m’gawo lathu?

3 Fufuzani Anthu Akhungu: Anthu akhungu sapezeka kaŵilikaŵili tikamacita ulaliki wa kunyumba ndi nyumba cifukwa ambili sakhala omasuka kulankhula ndi alendo amene afika pakhomo pao. Conco, pamafunika khama kuti ‘tifufuze’ anthu otelo n’colinga cakuti tiwalalikile. (Mat. 10:11) Kodi muli ndi mnzanu wa kunchito kapena wa kusukulu amene ndi wakhungu? Yambani kukamba naye. Ngati m’gawo lanu muli sukulu ya anthu akhungu, mungapemphe kuika zofalitsa zina za zilembo za akhungu m’laibulale ya pa sukulupo. Kodi mukudziŵako winawake amene m’banja lao muli munthu wakhungu? Kodi m’gawo lanu muli mabungwe othandiza anthu akhungu kapena nyumba zosungilamo anthu akhungu? Fotokozelani munthu wa m’banja lake, wolandila alendo, kapena owayang’anila kuti Mboni za Yehova ndi zofunitsitsa kuthandiza anthu akhungu, ndipo muuzeni kuti ndife okonzeka kumawabweletsela mabuku a anthu akhungu ndi nkhani zomvetsela cabe. Mufotokozeleni lonjezo la m’Baibulo lakuti posacedwapa Mulungu adzatsegula maso a anthu akhungu. Mungamuonetse vidiyo ya pa jw.org yamutu wakuti, “Without It, I Would Feel Lost,” (Popanda Baibulo, Sindikanadziŵa Ciliconse) imene imafotokoza za munthu wakhungu amene anapindula ndi Baibulo la zilembo za anthu akhungu. Kufotokoza cifukwa cimene mwafikila, kudzakuthandizani kupeza mwai woyamba kukambilana ndi anthu akhungu.

4. Kodi cocitika ca Janet cikutiphunzitsa ciani?

4 Mlongo wina wakhungu dzina lake Janet anapita kunyumba imene kumakhala anthu akhungu. Kumeneko iye anayamba kukambilana ndi mtsikana wina. Janet anauza mtsikanayo kuti: “Yesu anacilitsa akhungu n’colinga cakuti aonetse zimene adzacitila akhungu onse.” Iwo anakambilana lemba la Chivumbulutso 21:3, 4, ndipo Janet anafotokoza mmene lonjezo limeneli lidzakwanilitsidwila mu Ufumu wa Mulungu. Mtsikanayo anakhala cete pang’ono kenako anati: “Sindinamvepo wakhungu akunena zimenezi. Anthu ambili amakhulupilila kuti anthu ena ndi akhungu cifukwa ca zimene io kapena makolo ao akale analakwitsa.” Janet anatumizila mtsikanayo buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa m’zilembo za anthu akhungu pa kompyuta, ndipo tsopano amaphunzila Baibulo kaŵili pa mlungu.

5. Ngakhale kuti sitingacilitse munthu wakhungu monga mmene Yesu anacitila, kodi kuwacitila cifundo kungabweletse madalitso otani?

5 Ife sitingacilitse anthu akhungu monga mmene Yesu anacitila. Koma tingathandize anthu amene maganizo ao acititsidwa khungu ndi mulungu wa nthawi ino, kuphatikizapo anthu amene saona kuti amvetse coonadi ca Mau a Mulungu. (2 Akor. 4:4) Yesu “atagwidwa ndi cifundo,” anacilitsa amuna aŵili pafupi ndi Yeriko. (Mat. 20:34) Ngati tionetsa cifundo cofananaco tikakumana ndi munthu wakhungu, tidzasangalala kukhala ndi mwai wothandiza munthuyo kuphunzila za Yehova amene adzacititsa anthu akhungu kuyamba kuona.

Zimene Mungacite Pothandiza Munthu Wakhungu . . .

  • Kambani naye mwacindunji koma musalankhule mokweza mau. Ngakhale kuti anthu akhungu saona, io amamva bwinobwino.

  • Mugwileni dzanja ndipo mutsogoleleni. Iye adzakwanitsa kukutsatilani mukamayenda pang’onopang’ono patsogolo pake. Mukaona zinthu zimene zifunika kuzipewa, cingakhale bwino kumudziŵitsa.

  • Muzikhala omasuka kugwilitsila nchito mau otanthauza kuona monga akuti “onani”. Anthu akhungu naonso amawagwilitsila nchito. Iwo amatha kuona zinthu m’maganizo mwao ngakhalenso kupanga zithunzi za m’maganizo pa zinthu zimene mukukambapo.

  • Pokambilana muzikhala pa malo amene palibe phokoso. Anthu akhungu samasuka kukhala pa malo amene pali phokoso cifukwa amavutika kudziŵa zimene zikucitika pamalo amenewo.

  • Mukafuna kucoka muuzeni, kuopela kuti angazikamba ndi mphepo zimene zingamucititse manyazi.

  • Ngati munthu wakhungu waonetsa cidwi koma sakhala m’gawo lanu, lembani fomu ya Kaonaneni ndi Wacidwi Uyu (S-43) ndi kuipeleka kwa kalembela.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani