CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 44-45
Yosefe Anakhululukila Abale Ake
44:1, 2, 33, 34; 45:4, 5
Zingakhale zovuta kukhululuka, maka-maka ngati wina anaticitila zinthu zoipa mwadala. Kodi n’ciani cinathandiza Yosefe kukhululukila abale ake pamene anamucitila zinthu zoipa?
Yosefe sanafune kuwabwezela, m’malomwake anayetsetsa kuona ngati iwo anasintha popeza anali kufuna kuwakhululukila.—Sal. 86:5; Luka 17:3, 4
Yosefe sanapitilize kusunga cakukhosi, m’malomwake anatengela citsanzo ca Yehova amene amakhululukila na mtima wonse. —Mika 7:18, 19
Kodi ningatengele bwanji citsanzo ca Yehova pankhani yokhululukila ena?