CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 4-5
“Ine Ndidzakhala Nawe Polankhula”
4:10-15
Ndi thandizo la Yehova, Mose anagonjetsa mantha ake. Kodi tingaphunzilepo ciani pa zimene Yehova anauza Mose?
Tizipewa kusumika maganizo athu pa zinthu zimene timalephela kucita
Tiyenela kukhala na cidalilo cakuti Yehova adzatipatsa zonse zofunikila kuti tikwanilitse nchito imene tapatsidwa
Cikhulupililo cathu mwa Mulungu cidzatithandiza kuti tisamaope anthu
Kodi Yehova wanithandiza bwanji kupitiliza kulalikila ngakhale panthawi zovuta?