UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Tamandani Yehova Monga Mpainiya
Aisiraeli anali na zifukwa zabwino zotamandila Yehova. Iye anawatulutsa mu Iguputo na kuwapulumutsa kwa asilikali a Farao. (Eks. 15:1, 2) Yehova wapitiliza kucitila anthu ake zinthu zabwino. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife oyamikila?—Sal. 116:12.
Njila imodzi ni mwa kutumikila monga mpainiya wothandiza kapena wanthawi zonse. Mungapemphele kwa Mulungu kuti akupatseni mtima wofunitsitsa na mphamvu zoti mutumikile monga mpainiya. (Afil. 2:13) Ambili amayamba mwa kucitako upainiya wothandiza. Pocita utumiki waupainiya umenewu, mungasankhe kuthela maola 30 kapena 50 m’mwezi wa March na April, komanso m’mwezi umene woyang’anila dela acezela mpingo. Pambuyo poona cimwemwe cimene mwapeza cifukwa cotumikila monga mpainiya wothandiza, mwina mungafune kulimbikila kuti mutumikile monga mpainiya wanthawi zonse. Ngakhale ena amene agwila nchito yolembedwa kapena amene ali na vuto la thanzi akwanitsa kucita upaniya wanthawi zonse. (mwb16.07 8) Ndithudi timacita zonse zimene tingathe potamanda Yehova. Ndipo ni woyeneladi kutamandidwa.—1 Mbiri 16:25.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI ALONGO ATATU A PACIBALE KU MONGOLIA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi ni zopinga ziti zimene alongo atatu aja anagonjetsa kuti akhale apainiya?
Nanga ni madalitso otani amene anapeza?
Ni mwayi wa mautumiki uti umene anapeza pamene anali kutumikila monga apainiya anthawi zonse?
Kodi citsanzo cawo cinawakhudza motani ena?