Mipata Yoonjezeka Yotamanda Yehova
1. Kodi ndi makonzedwe atsopano ati amene adzatithandiza ‘kutamanda kwambili Yehova’?
1 Kuyambila mwezi wa March wapitawu, makonzedwe atsopano anayamba kugwila nchito. Makonzedwe amenewa azipatsa mwai ofalitsa kucita upainiya wothandiza wa maola 30 m’mwezi wa March ndi April komanso mwezi umene woyang’anila dela akucezela mpingo. Ngati kucezela kwa woyang’anila dela kukupitilila kufika m’mwezi wina, ofalitsa amene asankha kucita upainiya wa maola 30, azisankha mwezi umene angacite upainiya wothandiza. Apainiya onse othandiza azipezekapo pa msonkhano wonse umene woyang’anila dela amakhala nao ndi apainiya a nthawi zonse komanso apadela. Zimenezi zionetsa kuti ngati sitingakwanitse kucita upainiya wa maola 50, ‘tingatamandenso kwambili Yehova’ pocita upainiya wothandiza wa maola 30, kanai pa caka.—Sal. 109:30; 119:171.
2. Kodi amene adzacita upainiya wothandiza pa kucezela kwa woyang’anila dela adzasangalala ndi zotani?
2 Panthawi ya Kucezela kwa Woyang’anila Dela: Ambili adzatha kucita upainiya wothandiza panthawi ya kucezela kwa woyang’anila dela ndi kukhala ndi mwai wolimbikitsana pamene adzayenda naye pamodzi muulaliki. (Aroma 1:11, 12) Apainiya othandiza ambili adzakonza zakuti akapume tsiku limodzi mkati mwa mlungu n’colinga cakuti akagwile nchito pamodzi ndi woyang’anila dela. Amene amagwila nchito mkati mwa mlungu angapemphe woyang’anila dela ngati angapite naye muulaliki pa Ciŵelu kapena pa Sondo. Kuonjezela apo, apainiya othandiza adzalimbikitsidwa kwambili kupezeka pa msonkhano wa apainiya pamodzi ndi apainiya a nthawi zonse ndi apadela.
3. N’cifukwa ciani nyengo ya Cikumbutso ndi nthawi yabwino yocita upainiya wothandiza?
3 M’mwezi wa March ndi wa April: Ofalitsa amene anali kutengako mbali m’makonzedwe akale ocita upainiya wothandiza wa maola 30 m’nyengo ya Cikumbutso, tsopano angaonjezele nsembe yao ya citamando. (Aheb. 13:15) Mwezi wa March ndi wa April ndi miyezi yabwino kwambili yoonjezela utumiki wathu monga apainiya othandiza. Caka ciliconse miyezi imeneyi, timacita nchito yapadela yoitanila anthu ku Cikumbutso. Kuonjezela apo, popeza ambili amaonjezela utumiki wao pa nyengo ya Cikumbutso, tingapite mu ulaliki ndi ofalitsa osiyana-siyana. Pambuyo pa Cikumbutso, tiyenela kukulitsa cidwi ca anthu amene anapezekapo ndi kuwalimbikitsa kuti akabwelenso kudzamvetsela nkhani yapadela ya anthu onse. Kodi mtima wanu udzakulimbikitsani kuti mugwilitsile nchito mipata yoonjezeleka yocita upainiya wothandiza?—Luka 6:45.