LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 2/13 tsa. 1
  • Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza?
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • Pangani Nyengo Ino ya Cikumbutso Kukhala Yosangalatsa
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Mipata Yoonjezeka Yotamanda Yehova
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza m’Mwezi wa March Kapena April?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 2/13 tsa. 1

Kodi Mudzacitako Upainiya Wothandiza?

1. N’cifukwa ciani nyengo ya cikumbutso ndi nthawi yabwino yofutukula utumiki wathu?

1 Nyengo ya cikumbutso ndi nthawi yabwino yofutukula utumiki wathu. Nthawi imeneyi timaganizila za cikondi cacikulu cimene Yehova anaonetsa mwa kupeleka Mwana wake monga dipo. (Yoh. 3:16) Zimenezi zimaticititsa kukhala ndi ciyamikilo cacikulu m’mitima yathu, kukulitsa cifuno cathu couzako ena za Yehova ndi zimene akucitila mtundu wa anthu. (Yes. 12:4, 5; Luka 6:45) Nthawi imeneyi timakhalanso ndi mwai wapadela woitanila mabwenzi ndi anthu a m’gawo lathu kuti adzakhale nafe ku Cikumbutso. Pambuyo pa Cikumbutso timayesetsa kukulitsa cidwi ca aja amene anapezekapo. Kodi mudzafutukula utumiki wanu mwa kucitako upainiya wothandiza m’miyezi ya March, April, ndi May?

2. N’cifukwa ciani mwezi wa March ndi mwezi wabwino kucitako upainiya wothandiza?

2 Pangani Mwezi wa March Kukhala Wapadela: Mwezi wa March udzakhala wabwino kwambili kucitako upainiya wothandiza. Aja amene afunsila kucitako upainiya angasankhe kukwanilitsa maola 30 kapena 50. Ngati woyang’anila dela adzacezela mpingo wanu m’mwezi wa March, apainiya othandiza angapezekepo pa msonkhano wonse umene iye adzacita ndi apainiya a nthawi zonse ndi apadela. Mosiyana ndi zaka zakumbuyo, nthawi ya nchito yapadela yoitanila anthu ku Cikumbutso cimene cidzacitika pa Ciŵili pa March 26, 2013 yaonjezedwa ndipo idzayamba pa March 1. Ndipo mwezi wa March uli ndi milungu isanu. Bwanji osaganizilapo bwino kuti inunso mudzakhale mmodzi wa anthu amene adzapanga mwezi umenewu kukhala wapadela kwambili caka cino?

3. Kodi tingapange makonzedwe ati kuti tionjezele utumiki wathu?

3 Konzekelani Tsopano: Tsopano ndi nthawi yakuti muone ngati mungafunikile kusintha ndandanda yanu kuti mudzaciteko upainiya wothandiza. Muyenela kugwilizana monga banja, conco patulani nthawi pocita Kulambila kwa Pabanja kuti mukambilane zolinga zanu monga banja ndi kupanga ndandanda. (Miy. 15:22) Musataye mtima ngati simungathe kucitako upainiya wothandiza. Kodi simungasinthe ndandanda yanu kuti muonjezele nthawi pa masiku amene mumapita mu utumiki wakumunda? Kodi mungaonjezele tsiku limodzi kuti muzilalikila mkati mwa mlungu?

4. Kodi tidzapeza mapindu ati tikaonjezela utumiki wathu m’miyezi ya March, April, ndi May?

4 Pamene tionjezela utumiki wathu m’miyezi ya March, April, ndi May, tidzakhala acimwemwe ndiponso okhutila cifukwa cotumikila Yehova ndi kupatsa ena. (Yoh. 4:34; Mac. 20:35) Cofunika kwambili n’cakuti, tikapitiliza kudzipeleka mwakhama tidzasangalatsa Yehova.—Miy. 27:11.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani