Pangani Nyengo Ino ya Cikumbutso Kukhala Yosangalatsa
1. Kodi tingaonjezele bwanji cimwemwe cathu m’nyengo ya Cikumbutso?
1 Kodi mungakonde kuonjezela cimwemwe canu m’miyezi ya March, April, ndi May? Njila imodzi yocitila zimenezi ndi kucita zambili mu utumiki, ndipo ngati n’kotheka kucitako upainiya wothandiza. Kodi zimenezi zingaonjezele bwanji cimwemwe canu?
2. Kodi kucita zambili mu utumiki wathu kumaonjezela bwanji cimwemwe?
2 Onjezelani Cimwemwe Canu: Yehova anatilenga kuti tizisangalala pomulambila, ndipo mwacibadwa timafuna kukwanilitsa zosoŵa zathu za kuuzimu. (Mat. 5:3) Iye anatilenganso mwa njila yakuti tizipeza cimwemwe pamene tipatsa ena zinthu. (Mac. 20:35) Ulaliki umatipatsa mpata wocita zonse ziŵili, kulambila Mulungu ndi kuthandiza anthu. N’zomveka kuti tikaonjezela utumiki wathu m’pamene cimwemwe cathu cimaonjezeka. Ndiponso, pamene tithela nthawi yoculuka mu utumiki m’pamenenso cidziŵitso cathu cimaonjezeka kwambili. Cidziŵitso cathu cikaonjezeka, cidalilo cathu cimalimba ndipo mantha amacepa. Kenako timakhala ndi mipata yambili yolalikila ndi kuyambitsa maphunzilo a Baibulo. Zonsezi zimacititsa ulaliki kukhala wosangalatsa.
3. N’cifukwa ciani miyezi ya March ndi April idzakhala yabwino kucitako upainiya wothandiza?
3 Miyezi ya March ndi April idzakhala yabwino kwambili kucitako upainiya wothandiza cifukwa tingasankhe kukwanilitsa maola 30 kapena 50. Ndipo kuyambila pa Ciŵelu, March 22 mpaka pa tsiku la Cikumbutso pa Mande, April 14, tidzakhala ndi nchito yapadela yoitanila anthu ku Cikumbutso. Mipingo idzakhala yakali-yakali kugwila nchito “mogwilizana” kuti ifole gawo ndi kuyesetsa kulimaliza m’nyengo ya cikumbutso.—Zef. 3:9.
4. Ngati tifuna kucitako upainiya wothandiza, kodi tiyenela kucita ciani?
4 Yambani Kukonzekela: Ngati simunayambe kukonzekela, zingakhale bwino kupendanso ndandanda yanu ndi kuona ngati mungasinthe zina ndi zina kuti muonjezele utumiki wanu m’mwezi umodzi kapena ingapo. Ipempheleleni nkhaniyi. (Yak. 1:5) Kambitsilanani nkhaniyi ndi banja lanu ndi ena mumpingo. (Miy. 15:22) Mosasamala kanthu za thanzi lanu kapena ngati mulibe nthawi yambili, inunso mungakhale ndi cimwemwe cifukwa cocitako upainiya wothandiza.
5. Kodi kuonjezela utumiki wathu m’nyengo ino ya Cikumbutso kuli ndi ubwino wanji?
5 Yehova amafuna kuti atumiki ake azisangalala. (Sal. 32:11) Tikayesetsa kuonjezela utumiki wathu m’nyengo ino ya Cikumbutso, tidzaonjezela cimwemwe cathu komanso tidzasangalatsa Atate wathu wakumwamba.—Miy. 23:24; 27:11.