M’Nyengo Ino ya Cikumbutso, Kodi Mudzatengela Kudzipeleka kwa Yehova ndi Yesu?
1. Kodi Mboni za Yehova zimayesetsa kucita ciani pa nyengo ya Cikumbutso?
1 Yehova amakwanilitsa colinga cake modzipeleka. Lemba la Yesaya 9:7 limanena za madalitso ena a Ufumu wa Mulungu kuti: “Yehova wa makamu adzacita zimenezi modzipeleka kwambili.” Mofananamo, pa nthawi imene Mwana wa Mulungu anali kucita ulaliki wake padziko lapansi, anadzipeleka kwambili pa kulambila koona. (Yohane 2:13-17; 4:34) Caka ciliconse pa nyengo ya Cikumbutso, ofalitsa mamiliyoni ambili padziko lonse amacita khama kutsatila citsanzo ca kudzipeleka ca Yehova ndi Yesu mwa kuonjezela zocita zao mu ulaliki. Kodi inunso mudzacita zimenezo?
2. Kodi kudzipeleka kudzatilimbikitsa kucita ciani kuyambila pa March 7?
2 Kuitanila Anthu ku Cikumbutso: Caka cino nchito yoitanila anthu ku Cikumbumbutso idzayamba pa Ciŵelu pa March 7. Yambani tsopano kukonzekela kuti mudzagwileko nchito imeneyi mokwanila. Mipingo idzasangalala kwambili kugwila nchito yoitanila anthu ku Cikumbutso m’gawo lao. Muyenela kuyesetsa kudzaitana amene mumaphunzila nao Baibulo, acibale, anzanu akunchito, a kusukulu, amene mumacitako maulendo obwelelako ndi anthu ena. Mungacite zimenezi mwa kuwapatsa kapepala kapena kugwilitsila nchito webusaiti yathu ya jw.org.
3. Tingaonjezele bwanji utumiki wathu m’miyezi ya March ndi April?
3 Upainiya Wothandiza: Kudzipeleka kudzatilimbikitsanso kuonjezela utumiki wathu. Mosakaikila ambili adzakwanitsa kucita upainiya wothandiza m’miyezi ya March ndi April, popeza kuti tidzakhala ndi mwai wosankha kucita upainiya wa maola 30 kapena kuposapo. Pa kulambila kwanu kwa pabanja kapena pa phunzilo laumwini, mungaganizile mwapemphelo za mmene mungaonjezelele utumiki wanu. (Miy. 15:22) Citsanzo canu ca kudzipeleka pa nchito yapadela imeneyi cidzalimbikitsa ena kugwila nchitoyi modzipeleka. Ngati mungasinthe zinthu zina ndi zina paumoyo wanu kuti mucite zambili, mudzakhala mukutsatila citsanzo ca Yesu ca kukhala wodzipeleka.—Maliko 6:31-34.
4. Ndi madalitso otani amene timapeza cifukwa cotsatila citsanzo ca kudzipeleka ca Yehova ndi Yesu?
4 Kutsatila citsanzo ca kudzipeleka ca Yehova ndi Yesu pa nyengo iyi ya Cikumbutso, kudzacititsa kuti tilandile madalitso ambili. Anthu ambili m’gawo lathu adzalandila uthenga wabwino. Tidzakhala ndi cimwemwe cimene cimabwela cifukwa ca kutumikila Yehova ndiponso kupatsa ena. (Mac. 20:35) Koposa zonse, tidzasangalatsa Mulungu wathu ndi Mwana wake amene ndi odzipeleka.