Ndandanda ya Mlungu wa February 24
MLUNGU WA FEBRUARY 24
Nyimbo 101 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 5 ndime 1 mpaka 6, ndi bokosi patsamba 55 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Genesis 32-35 (Mph. 10)
Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 96
Mph. 5: Kuyambitsa Phunzilo la Baibulo pa Ciŵelu Coyamba. Nkhani. Chulani makonzedwe a ulaliki amene mpingo wapanga pa Ciŵelu coyamba mu March. Citani citsanzo cimene cili patsamba 4.
Mph. 15: Cifukwa Cake Kulimbikila N’kofunika. Nkhani yokambitsilana yocokela mu Buku Lapacaka la 2013 tsamba 45, ndime 1, mpaka tsamba 46, ndime 1; ndi masamba 136 mpaka 137. Pemphani omvela kuti afotokoze zimene aphunzilapo.
Mph. 10: “Tidzayamba Kuitanila Anthu ku Cikumbutso pa March 22.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anila nchito. Gaŵilani tumapepala toitanila anthu ku Cikumbutso ndi kukambitsilana mfundo zake. Bwelelani m’malangizo othandiza a m’kalata ya akulu, ndi kuchula makonzedwe a mpingo ofola gawo lonse.
Nyimbo 109 ndi Pemphelo