Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa February 24, 2014.
1. Kodi Satana anacititsa Hava kuganizila kwambili zinthu ziti? Ndipo Hava anaonetsa ciani pamene anadya cipatso coletsedwa? (Gen. 3:6) [January 6, w11 5/15 tsa. 16-17 ndime 5]
2. Kodi n’ciani cinathandiza Abele kukhala ndi cikhulupililo colimba? Ndipo cotsatilapo cake cinali ciani? (Gen. 4:4, 5; Aheb. 11:4) [January 6, w13 1/1 tsa. 12 ndime 3 ndi tsa. 14 ndime 4-5]
3. Kodi makolo angathandize bwanji ana ao kuti asatengele makhalidwe oipa a anthu amphamvu ndi “ochuka” a m’dzikoli? (Gen. 6:4) [January 13, w13 4/1 tsa. 13 ndime 2]
4. Kodi tiphunzilapo ciani pankhani ya Loti ndi mkazi wake yolembedwa pa Genesis 19:14-17, andi 26? [January 27, w03 1/1 tsa. 16-17 ndime 20]
5. Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali ndi cikhulupililo cakuti akufa adzaukitsidwa, ndi kuti lonjezo la Yehova lakuti mwana adzacokela mwa Isaki lidzakwanilitsidwa? (Gen. 22:1-18) [February 3, w09 2/1 tsa. 18 ndime 4]
6. Kodi ulosi wopezeka pa Genesis 25:23 wakuti “wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono,” umatiphunzitsa mfundo zofunika ziti? [February 10, w03 10/15 tsa. 29 ndime 2]
7. Kodi loto la Yakobo lokhudza makwelelo linatanthauza ciani? (Gen. 28:12, 13) [February 10, w04 1/15 tsa. 28 ndime 6]
8. N’cifukwa ciani Labani anafunitsitsa kupeza aterafi amene anabedwa? (Gen. 31:30-35) [February 17, w04 6/1 tsa. 29 ndime 2]
9. Kodi yankho limene mngelo anapeleka kwa Yakobo pa Genesis 32:29 limatiphunzitsa ciani? [February 24, w13 8/1 tsa. 10]
10. Kodi tingacite bwanji kuti tipewe mavuto monga amene anagwela Dina? (Gen. 34:1, 2) [February 24, w01 8/1 mas. 20-21]