Ndandanda ya Mlungu wa March 3
MLUNGU WA MARCH 3
Nyimbo 112 ndi Pemphelo
□ Phunzilo la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 5 ndime 7 mpaka 12 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Ulaliki:
Kuŵelenga Baibulo: Genesis 36-39 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 37:1-17 (Mph. 4 kapena zocepelapo)
Na. 2: Cifukwa Cimene Anthu Oukitsidwa Sadzalangidwila Nchito Zao Zakale—rs tsa. 111 ndime 4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Akristu Angaphunzile Ciani kwa Abigayeli?—1 Samueli 25:14-35 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Nchito:
Nyimbo 117
Mph. 10: Kugaŵila Magazini mu March. Nkhani yokambitsilana. Yambani mwa kucita citsanzo ca mmene mungagaŵilile magazini mwa kugwilitsila nchito ulaliki wacitsanzo patsamba lino. Ndiyeno kambitsilanani ulaliki wonse kucokela kuciyambi mpaka kumapeto. Malizani mwa kupempha omvetsela kuti afotokoze mmene angagaŵilile magazini pamodzi ndi kapepala ka ciitano kumapeto kwa milungu iŵili yomaliza ya mwezi uno.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinacita Bwanji Mwezi Watha? Nkhani yokambitsilana. Pemphani ofalitsa kuti afotokoze mmene apindulila pogwilitsila nchito mfundo za m’nkhani yakuti, “Kuongolela Luso Lathu mu Ulaliki—Tizilemba Tikapeza Anthu Acidwi.” Pemphani omvela kuti afotokoze zocitika zosangalatsa za mu ulaliki.
Nyimbo 95 ndi Pemphelo