CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKSODO 19–20
Mfundo za Malamulo Khumi Zotithandiza
20:3-17
Akhristu sali pansi pa Cilamulo ca Mose. (Akol. 2:13, 14) Ndiyeno kodi Malamulo Khumi na malamulo ena onse a m’Cilamulo amatithandizabe motani masiku ano?
Amatithandiza kudziŵa mmene Yehova amaonela nkhani zina
Amationetsa zimene Yehova amatiyembekezela kucita kuti timukondweletse
Amationetsa mmene tifunika kucitila zinthu na anthu ena
Kodi Tiphunzila Ciani za Yehova Kucokela ku Malamulo Khumi?