UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pewani Kufalitsa Nkhani Zabodza
Masiku ano, nkhani zimafalikila mwamsanga kwa anthu mamiliyoni ambili kupitila m’zopulinta, pa wailesi, pa TV, komanso pa Intaneti. Anthu amene amalambila “Mulungu wacoonadi” amayesetsa kupewa kufalitsa nkhani zabodza, ngakhale mosadziŵa. (Sal. 31:5; Eks. 23:1) Kuuza anthu ena nkhani yabodza kungakhale kovulaza kwambili. Pofuna kutsimikizila ngati nkhani inayake ni yazoona, dzifunseni kuti:
‘Kodi magwelo a nkhaniyi ni odalilika?’ Munthu amene akutiuza nkhani sangadziŵe zeni-zeni zokhudza nkhaniyo. Nkhani zimene zimacoka kwa munthu wina kupita kwa wina nthawi zina zimasintha, conco tifunika kukhala osamala ngati sitidziŵa kumene nkhaniyo inacokela kapena kumene inayambila. Popeza amene ali na maudindo mu mpingo ndiwo gwelo la nkhani zodalilika, iwo afunika kukhala osamala kwambili pankhani youza ena zinthu zopanda umboni.
‘Kodi ni misece?’ Ngati nkhaniyo ni yoipitsa mbili ya munthu wina kapena gulu, n’canzelu kupewa kuuzako ena.—Miy. 18:8; Afil. 4:8.
‘Kodi nkhaniyi ni yazoona?’ Khalani maso pamene mumvela nkhani zokopa.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI KODI NINGAKANIZE BWANJI MIJEDO? NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Malinga na Miyambo 12:18, kodi mawu athu angavulaze ena motani?
Kodi Afilipi 2:4 ingatithandize bwanji kuti tizikamba zinthu zoyenela zokhudza anthu ena?
Kodi tifunika kucita ciani pamene ena ayamba kukamba nkhani zolakwika zokhudza anthu ena?
Tisanayambe kukamba zokhudza ena, ni mafunso ati amene tifunika kudzifunsa?