CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | EKSODO 25-26
Cimene Cinali Cofunika Kwambili m’Cihema
25:9, 21, 22
Likasa linali cinthu cofunika kwambili m’cihema komanso mu msasa wa Aisiraeli. Kukhalapo kwa Mulungu kunali kuimilidwa na mtambo umene unali pakati pa akelubi, amene anali pa civundikilo ca likasa. Caka ciliconse, pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, mkulu wa ansembe anali kuloŵa m’malo Oyela Koposa ndipo anali kudontheza magazi a ng’ombe yamphongo na mbuzi patsogolo pa civundikilo kuti aphimbe macimo ya Aisiraeli. (Lev. 16:14, 15) Izi zinali kuimila nthawi pamene Mkulu wa Ansembe Yesu, analowa kumwamba kukapeleka mtengo wake wa dipo pamaso pa Yehova.—Aheb. 9:24-26.
Gwilizanitsani malemba otsatilawa na mapindu amene tili nawo cifukwa ca nsembe:
MALEMBA
1 Yoh. 1:8, 9
Aheb. 9:13, 14
MAPINDU
ciyembekezo ca moyo wosatha
kukhululukidwa macimo
cikumbumtima coyela
Kodi tifunika kucita ciani kuti tipeze mapindu amenewa?