LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb20 December tsa. 3
  • Timaonetsa Cikondi Ngati Ticita Zinthu Mogwilizana na Cilango ca Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Timaonetsa Cikondi Ngati Ticita Zinthu Mogwilizana na Cilango ca Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Cilango Cimaonetsa Cikondi ca Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Cifukwa Cake Kucotsa Munthu Mumpingo Ndi Makonzedwe Acikondi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Munthu Amene Timakonda Akasiya Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Cilango Ni Umboni Wakuti Mulungu Amatikonda
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
mwb20 December tsa. 3

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Timaonetsa Cikondi Ngati Ticita Zinthu Mogwilizana na Cilango ca Yehova

Kucotsa mu mpingo anthu olakwa osalapa kumateteza mpingo, komanso ni cilango kwa anthu osalapawo. (1 Akor. 5:6, 11) Tikamacita zinthu mogwilizana na cilango ca Yehova cimeneci, timaonetsa kuti tili na cikondi. N’cifukwa ciani takamba conco pamene kucotsa munthu mu mpingo kumabweletsa cisoni kwa onse okhudzidwa, kuphatikizapo acibale apafupi komanso abale a m’komiti yaciweluzo?

Cacikulu kuposa zonse n’cakuti, ngati ticita zinthu mogwilizana na cilango ca Yehova, timaonetsa kuti timakonda dzina lake na miyezo yake yoyela. (1 Pet. 1:14-16) Timaonetsanso cikondi kwa wocotsedwayo. Zili conco cifukwa cilango camphamvu, olo cikhale cowawa, cingabale “cipatso camtendele comwe ndi cilungamo.” (Aheb. 12:5, 6, 11) Ngati tiyanjana na munthu wocotsedwa kapena wodzilekanitsa, timalepheletsa cilango ca Yehova kugwila nchito bwino. Kumbukilani kuti Yehova amalanga anthu ake “pa mlingo woyenela.” (Yer. 30:11) Timakhala na ciyembekezo cakuti munthu amene wacotsedwa adzabwelela kwa Atate wathu wacifundo. Koma palipano, timapitiliza kucita zinthu mogwilizana na cilango ca Yehova na kuyesetsa mmene tingathele kulimbitsa ubale wathu na Yehova.—Yes. 1:16-18; 55:7.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI KHALANIBE OKHULUPILIKA NA MTIMA WONSE, NDIPO PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti ‘Khalanibe Okhulupilika na Mtima Wonse.’ Gabriella na Ben akulila ataŵelenga kalata yocokela kwa mwana wawo wamwamuna amene anacoka pakhomo.

    Kodi makolo acikhristu amamvela bwanji ngati mwana wawo wasiya Yehova?

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti ‘Khalanibe Okhulupilika na Mtima Wonse.’ Mabwenzi akumbatila na kutonthoza Gabriella na Ben pambuyo pa msonkhano wa mpingo.

    Kodi mpingo ungawathandize bwanji acibale okhulupilika a munthu wocotsedwa?

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti ‘Khalanibe Okhulupilika na Mtima Wonse.’ Gabriella akusinkha-sinkha nkhani ya kupanduka kwa Kora.

    Ni nkhani iti ya m’Baibo imene imaonetsa kufunika kokhala wokhulupilika kwambili kwa Yehova kuposa kwa acibale athu?

  • Cithunzi ca mu vidiyo yakuti ‘Khalanibe Okhulupilika na Mtima Wonse.’ Pambuyo pa msonkhano, Gabriella akuuza mwamuna wake Ben za meseji imene walandila kucokela kwa mwana wawoyo.

    Timaonetsa bwanji kuti ndife okhulupilika kwambili kwa Yehova kuposa kwa acibale athu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani