LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 March tsa. 9
  • Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Khalanibe Okhulupilika Pamene M’bululu Wanu Wacotsedwa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 March tsa. 9
Nthaka ikung’ambika na kumeza Aisiraeli opanduka.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika

Kora, Datani na Abiramu anaonetsa kusakhulupilika kwa Yehova mwa kupandukila makonzedwe ake. Yehova anawononga opandukawo na onse amene anali ku mbali yawo. (Num. 16:26, 27, 31-33) Ni zocitika monga ziti zimene zingayese kukhulupilika kwathu kwa Yehova? Ni zitsanzo ziti za m’Baibo zimene zingatithandize kuti tisatengele anthu osakhulupilika?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEWANI KUTENGELA ANTHU OSAKHULUPILIKA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Mbali ya vidiyo yakuti, ‘Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika.’ Nadi akuyelekeza kuti akuona mnyamata akumupatsa botolo la moŵa ku phwando lacongo.

    Ni cocitika citi cimene cinayesa kukhulupilika kwa Nadi? Nanga ni citsanzo citi coticenjeza cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika?

  • Mbali ya vidiyo yakuti, ‘Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika.’ M’bale wokhumudwa akuganizila nkhani imene ikumuvutitsa maganizo.

    Ni cocitika cotani cimene cinayesa kukhulupilika kwa m’bale amene anakhumudwa? Nanga ni citsanzo citi coticenjeza cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika?

  • Mbali ya vidiyo yakuti, ‘Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika.’ M’bale Elliott akuyelekeza kuti akukambilana aŵili-ŵili na mlongo wosudzulidwa pa malo oika mamotoka ku Nyumba ya Ufumu.

    N’ciani cinayesa kukhulupilika kwa m’bale Elliott? Nanga ni citsanzo citi coticenjeza cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika?

  • Mbali ya vidiyo yakuti, ‘Pewani Kutengela Anthu Osakhulupilika.’ M’bale wacinyamata akuona linki yopitila pa webusaiti ya njuga imene mnzake wamutumila pa foni.

    N’ciani cinayesa kukhulupilika kwa m’bale wina kusukulu? Nanga ni citsanzo citi coticenjeza cimene cinamuthandiza kukhalabe wokhulupilika?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani