LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 March tsa. 13
  • Seŵenzetsani Mawu a Mulungu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Seŵenzetsani Mawu a Mulungu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Funsani Mafunso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Afikeni Pamtima Anthu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Landilani Thandizo la Yehova Kupitila M’pemphelo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 March tsa. 13

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Seŵenzetsani Mawu a Mulungu

Mawu a Mulungu ni amphamvu! (Aheb. 4:12) Angafike pamtima ngakhale anthu amene sadziŵa Mulungu. (1 Ates. 1:9; 2:13) Timapeza cimwemwe cacikulu ngati winawake wakondwela na mfundo inayake ya coonadi ca m’Baibo imene tamuonetsa.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—LOLANI MPHAMVU YA MAWU A MULUNGU KUGWILA NCHITO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Lolani Mphamvu ya Mawu a Mulungu Kugwila Nchito.’ Neeta amvetsela pamene Rose aŵelenga lemba.

    Kodi mlongo Neeta walola bwanji mphamvu ya Mawu a Mulungu kugwila nchito pothandiza Rose kuona kufunika kofufuza m’Mawu a Mulungu?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti, ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Lolani Mphamvu ya Mawu a Mulungu Kugwila Nchito.’ Rose aŵelenga lemba mokweza.

    Kodi Neeta walola bwanji mphamvu ya Mawu a Mulungu kugwila nchito mwa kuŵelenga lemba mokweza na kufotokoza cabe mfundo yofunika pa lembalo?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Lolani Mphamvu ya Mawu a Mulungu Kugwila Nchito.’ Rose amwetulila pamene ayang’ana Neeta.

    N’ciani cimene cionetsa kuti lemba lamufika pamtima Rose? Nanga muona kuti zimenezi zamukhudza bwanji Neeta?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani