LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 July tsa. 9
  • Afikeni Pamtima Anthu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Afikeni Pamtima Anthu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Funsani Mafunso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Seŵenzetsani Mawu a Mulungu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Landilani Thandizo la Yehova Kupitila M’pemphelo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Thandizani Maphunzilo a Baibo Kuleka Makhalidwe Odetsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 July tsa. 9

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Afikeni Pamtima Anthu

Mtima ndiwo umasonkhezela munthu kumvela Mulungu. (Miy. 3:1) Conco pamene tikuphunzitsa munthu, tiyenela kuyesetsa kumufika pamtima. Motani?

Sitiyenela kungophunzitsa wophunzila mfundo za coonadi ca m’Baibo. Koma tiyenelanso kum’thandiza kuona mmene mfundozo zimakhudzila umoyo wake komanso ubale wake na Yehova. M’thandizeni kuona kuti miyezo ya m’Baibo imaonetsa cikondi ca Mulungu, ubwino wake, na cilungamo cake. M’funseni mafunso mwaluso komanso mokoma mtima kuti mum’thandize kupendanso bwino mmene amaonela mfundo zimene akuphunzila. M’thandizeni kuganizila mapindu amene adzapeza akasintha maganizo ake olakwika na zizoloŵezi zoipa. Mukaona kuti wophunzila wayamba kukonda Yehova na mtima wonse, cimwemwe canu cidzawonjezeka.

ONELELANI VIDYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUWAFIKA PAMTIMA ANTHU. KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuwafika Pamtima Anthu.’ Neeta akufunsa funso Rose pa phunzilo lawo la Baibo.

    N’cifukwa ciani Neeta anafunsa Rose kuti: “Kodi unaiganizilaponso nkhani ija tinakambilana pa Mande?”

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuwafika Pamtima Anthu.’ Neeta akufotokozela Malemba.

    Kodi Neeta anamuthandiza bwanji Rose kuzindikila kuti miyezo ya m’Baibo imaonetsa kuti Yehova amamukonda?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuwafika Pamtima Anthu.’ Rose amvetsela pamene Neeta akamba.

    Tikamufika pamtima wophunzila wathu, tidzamusonkhezela kupita patsogolo

    Kodi Neeta anamuthandiza bwanji Rose kuganizila mmene angaonetsele kuti amakonda Mulungu?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani