LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsa. 5
  • Seŵenzetsani Mafanizo Pofotokoza Mfundo Zazikulu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Seŵenzetsani Mafanizo Pofotokoza Mfundo Zazikulu
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Mafanizo Ophunzitsadi Kanthu
    Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa
  • Landilani Thandizo la Yehova Kupitila M’pemphelo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Seŵenzetsani Mawu a Mulungu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Funsani Mafunso
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 May tsa. 5
Mayi na mwana wake wamkazi akuyang’anitsitsa mbalame na maluŵa pamene amvetsela kwa Yesu pa ulaliki wake wa pa phili.

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Seŵenzetsani Mafanizo Pofotokoza Mfundo Zazikulu

Popanga maulendo obwelelako kapena potsogoza maphunzilo a Baibo, tifunika kuthandiza omvela athu kumvetsetsa mfundo zazikulu. Tingacite bwanji zimenezi? Tiyenela kuseŵenzetsa mafanizo. Tikatelo, tidzawafika pamtima omvela, komanso tidzawathandiza kumakumbukila mfundo zimene tawaphunzitsa.

Pamene mukonzekela ulendo wobwelelako kapena kukatsogoza phunzilo la Baibo, onani mfundo zazikulu zimene mufuna kukafotokoza poseŵenzetsa mafanizo, osati mfundo zing’ono-zing’ono. Ndiyeno pezani mafanizo osavuta kumva ozikidwa pa zocitika za tsiku na tsiku. (Mat. 5:14-16; Maliko 2:21; Luka 14:7-11) Muyenelanso kuganizila cikhalidwe na zocitika za pa umoyo wa womvela wanu. (Luka 5:2-11; Yoh. 4:7-15) Mudzapeza cimwemwe poona kuti womvela wanu akukondwela na mfundo imene mwamuthandiza kumvetsetsa.

ONETSANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUSEŴENZETSA MAFANIZO POFOTOKOZA MFUNDO ZOFUNIKA KWAMBILI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuseŵenzetsa Mafanizo Pofotokoza Mfundo Zofunika Kwambili.’ Rose afunsa funso Neeta.

    N’cifukwa ciani ophunzila Baibo amafunika kuwathandiza kuti amvetsetse mavesi a m’Baibo?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuseŵenzetsa Mafanizo Pofotokoza Mfundo Zofunika Kwambili.’ Neeta akuuza Rose fanizo.

    Kodi mlongo Neeta waseŵenzetsa bwanji fanizo pofotokoza mfundo ya coonadi ya pa Aroma 5:12?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Nolani Maluso Anu—Kuseŵenzetsa Mafanizo Pofotokoza Mfundo Zofunika Kwambili.’ Neeta akuonetsa Rose vidiyo.

    Mafanizo abwino amawafika pamtima omvetsela

    Kodi mafanizo abwino angawakhudze bwanji omvela athu?

  • N’cifukwa ciani mu ulaliki tiyenela kuseŵenzetsa mavidiyo na zida zina zophunzitsila zimene gulu la Yehova latipatsa?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani