LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsa. 13
  • Onetsani Cikondi m’Banja

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Onetsani Cikondi m’Banja
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Zimene Muyenela Kucita Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Nzelu Zotithandiza Kukhala na Banja Lacimwemwe
    Galamuka!—2021
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
mwb21 May tsa. 13
Banja likuimbila pamodzi nyimbo pamsonkhano.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Onetsani Cikondi m’Banja

Cikondi cili ngati guluu. Cimagwilizanitsa banja. Popanda cikondi, m’banja simungakhale mgwilizano. Kodi amuna, akazi, na makolo angaonetse bwanji cikondi m’banja?

Mwamuna wacikondi amaganizila zosoŵa za mkazi wake, maganizo ake, komanso mmene amamvelela. (Aef. 5:28, 29) Amasamalila banja lake kuthupi na kuuzimu kuphatikizapo kucititsa Kulambila kwa Pabanja nthawi zonse. (1 Tim. 5:8) Mkazi wacikondi amagonjela mwamuna wake na ‘kumulemekeza kwambili.’ (Aef. 5:22, 33; 1 Pet. 3:1-6) Mwamuna na mkazi wake, ayenela kukhala okonzeka kukhululukilana na mtima wonse. (Aef. 4:32) Makolo acikondi amaonetsa cidwi kwa mwana aliyense, ndiponso amaphunzitsa ana awo kukonda Yehova. (Deut. 6:6, 7; Aef. 6:4) Amadzifunsa kuti, ‘Kodi ana athu amakumana na mavuto otani kusukulu? Kodi amacita bwanji ngati anzawo awanyengelela kucita zolakwika?’ Ngati m’banja muli cikondi, onse amadziona kuti ni otetezeka.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ONETSANI CIKONDI COSATHA M’BANJA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Onetsani Cikondi Cosatha M’banja.’ Atabwelela kunyumba pambuyo pa msonkhano, mwamuna na mkazi wake akukambilana lemba.

    Kodi mwamuna wacikondi amadyetsa bwanji mkazi wake kuuzimu na kuthupi komanso kumuonetsa cikondi?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Onetsani Cikondi Cosatha M’banja.’ Atabwelela kunyumba pambuyo pa msonkhano, mlongo amvetsela mwamuna wake amene si Mboni moleza mtima na kumutsimikizila kuti amamukonda.

    Kodi mkazi wacikondi amaonetsa bwanji kuti amam’lemekeza kwambili mwamuna wake?

  • Cithunzi coonetsa zocitika za mu vidiyo yakuti ‘Onetsani Cikondi Cosatha M’banja.’ Banja likambilana mfundo zimene asangalala nazo kumsonkhano pamene akudya zakudya zopepuka.

    Kodi makolo acikondi amakhomeleza bwanji Mawu a Mulungu mwa ana awo?

SAMALANI POSEŴENZETSA ZIPANGIZO ZAMAKONO

Ngati sitingasamale, zipangizo zamakono zingatiwonongele nthawi yoyenela kuseŵenzetsa polimbitsa cikondi m’banja. Makolo angaike malile pa nthawi imene iwo na ana awo ayenela kuthela poseŵenzetsa zipangizo zamakono. Makolo ayenela kuona ngati m’poyenela kuti ana awo acicepele aziceza ndi anthu pa intaneti, komanso kuti ni anthu otani amene angaceze nawo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani