CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI
Thandizani Maphunzilo a Baibo Kukhala pa Ubale Wolimba na Yehova
Yehova amafuna kuti tizim’tumikila cifukwa com’konda. (Mat. 22:37, 38) Kukonda Mulungu n’kumene kudzalimbikitsa ophunzila Baibo kupanga masinthidwe ofunikila, na kukhalabe olimba akakumana na mayeso. (1 Yoh. 5:3) Cikondi cawo pa Mulungu n’cimene cidzawalimbikitsa kuti abatizike.
Thandizani ophunzila anu kuona kuti Mulungu amawakonda. Afunseni mafunso monga awa: “Kodi izi zikuphunzitsani ciani za Yehova?” kapena “Kodi izi zimaonetsa bwanji kuti Mulungu amakukondani?” Athandizeni kuona mmene Yehova akuwathandizila pa umoyo wawo. (2 Mbiri 16:9) Auzeni mmene Yehova wayankhila mapemphelo anu acindunji, ndipo alimbikitseni kuona mmene Yehova amayankhila mapemphelo awo. Timakondwela kuona kuti ophunzila Baibo ayamba kumva kuti Yehova amawakonda, ndipo nawonso akuonetsa cikondi cawo pa iye.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI THANDIZANI MAPHUNZILO ANU A BAIBO KUKHALA PA UBALE WOLIMBA NA YEHOVA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:
Ni copinga cotani cimene Rose anakumana naco?
Kodi Neeta anam’thandiza bwanji Rose?
Kodi Rose anakwanitsa bwanji kugonjetsa copingaco?