LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb22 September tsa. 5
  • Ukwati Ni Mgwilizano wa Moyo Wonse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ukwati Ni Mgwilizano wa Moyo Wonse
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Umbeta na Ukwati?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Cikwati Ndi Mphatso Yocokela kwa Mulungu Wacikondi
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Cikwati Ni Mphatso Yocokela Kwa Mulungu
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Pambuyo Pa Tsiku La Cikwati
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
mwb22 September tsa. 5
M’bale na mkazi wake ali mu ulaliki.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Ukwati Ni Mgwilizano wa Moyo Wonse

Banja lacikhristu likamayenda bwino, Yehova amalemekezeka komanso aŵili okwatilanawo amakhala acimwemwe. (Maliko 10:9) Kuti Akhristu akakhale na banja lolimba komanso lacimwemwe, amafunika kutsatila mosamala mfundo za m’Baibo posankha woloŵa naye m’banja.

Muyenela kuyamba cibwenzi kokha ngati mwapitilila “pacimake pa unyamata,” cifukwa pa nthawiyi cilakolako ca kugonana cimakhala camphamvu kwambili ndipo cingakulepheletseni kusankha mwanzelu. (1 Akor. 7:36) Gwilitsani nchito mwanzelu nthawi ya umbeta polimbitsa ubale wanu na Mulungu, komanso kukulitsa makhalidwe acikhristu. Mukatelo, ndiye kuti mukakaloŵa m’banja, mudzathandiza kwambili kuti banjalo likakhala lolimba.

Musanagwilizane zokwatilana na munthu winawake, muyenela kukhala na nthawi yokwanila yodziŵa umunthu wake “wobisika wa mumtima.” (1 Pet. 3:4) Ngati pali zinthu zina zodetsa nkhawa zimene mwaona, kambilanani naye munthuyo. Monga zimakhalila na maunansi ena pakati pa anthu, ngati mwaloŵa m’banja, mumafunika kuika maganizo pa zimene mungacitile mnzanuyo, osati pa zimene mufuna kuti iye akucitileni. (Afil. 2:3, 4) Mukamatsatila mfundo za m’Baibo musanaloŵe m’banja, ndiye kuti mukuyala maziko olimba a banja lacimwemwe.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KUKONZEKELA KULOŴA M’BANJA—MBALI 3: KUWELENGELA MTENGO WAKE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi cibwenzi ca mlongoyu na Shane cinali kuyenda bwanji?

  • N’ciyani cimene mlongoyu anaona m’kupita kwa nthawi?

  • Kodi makolo ake anamuthandiza bwanji? Nanga iye anapanga cisankho cotani canzelu?

M’bale amene ali pa cibwenzi na mlongo angacite bwino kuganizila mafunso awa:

Kodi mlongoyu ali na makhalidwe ati abwino? Nanga amaonetsa bwanji kuti amaika zinthu za Ufumu patsogolo? Kodi amatsatila malangizo a m’Baibo komanso amene gulu limapeleka? Kodi ni woganizila ena?

Mlongo amene ali pa cibwenzi na m’bale angacite bwino kuganizila mafunso awa:

Kodi m’baleyu ali na makhalidwe ati abwino? Kodi amaika zinthu zauzimu komanso maudindo ake mumpingo patsogolo pa nchito, ndalama, maseŵelo, kapena zosangalatsa zina? Kodi a m’banja mwake amacita nawo zinthu motani? Kodi ni woganizila ena?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani