CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kucita Zinthu na Mtima Wonse Kumabweletsa Madalitso Oculuka
Elisa anauza Mfumu Yehoasi kuti acite cina cake coonetsa mmene Aisiraeli adzagonjetsela Asiriya (2 Maf. 13:15-18)
Yehoasi sanacite zinthu na mtima wonse. Ndiye cifukwa cake sanapambane kwenikweni polimbana na adani ake (2 Maf. 13:19; w10 4/15 26 ¶11)
Yehova amawadalitsa kwambili atumiki ake amene amam’funafuna na mtima wonse (Aheb. 11:6; w13 11/1 11 ¶5-6)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimaonetsa bwanji kuti nimacita zonse zimene ningathe pa zinthu zokhudza kulambila monga kuŵelenga Baibo, kupezeka ku misonkhano, na kulalikila?’