CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kuleza Mtima kwa Yehova Kuli na Malile
Yehova analola Asuri kugonjetsa Aisiraeli (2 Maf. 17:5, 6; it-2 908 ¶5)
Yehova anawalanga anthu ake cifukwa anapitiliza kucita zinthu zoipa zomukwiyitsa (2 Maf. 17:9-12; it-1 414-415)
Yehova anawalezela mtima Aisiraeli, ndipo anawacenjeza mobweleza-bweleza (2 Maf. 17:13, 14)
Atate wathu wacikondi wakumwamba ni woleza mtima kwambili na anthu opanda ungwilo. (2 Pet. 3:9) Ngakhale n’conco, kuti akwanilitse colinga cake, posacedwapa adzawononga anthu oipa. N’cifukwa ciyani zimenezi ziyenela kutilimbikitsa kumvela uphungu na kulalikila mwacangu?