UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Konzekelani Palipano Musanadwale Mwadzidzidzi Kapena Kukumana na Ngozi
N’cifukwa ciyani kukonzekela n’kofunika? Munthu aliyense angadwale mwadzidzidzi kapena kucita ngozi mpaka kugonekedwa m’cipatala. Conco, musanakumane na vuto lamwadzidzidzi, konzekelani bwino lomwe kuti zotelo zikadzacitika, mudzalandile cithandizo cabwino koposa ca mankhwala. Mukacita zimenezi, mudzaonetsa kuti mumalemekeza moyo komanso lamulo la Yehova pa nkhani ya magazi.—Mac. 15:28, 29.
Kodi mungakonzekele bwanji?
Pemphelani na kulemba bwino lomwe Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhila Thandizo la Mankhwala (DPA).a Ofalitsa obatizika angapemphe okha khadi la DPA kwa mtumiki wa mabuku, kuphatikizapo khadi la ana awo aang’ono lochedwa Identity Card (ic)
Ngati muli na pathupi, pemphani akulu kuti akupatseni fomu yakuti Mfundo Zokhudza Azimayi Apathupi (S-401). Fomu imeneyi idzakuthandizani kusankha bwino cithandizo ca mankhwala pa zovuta zimene zimakhalapo poyembekezela kucila ngakhale pocila kumene
Ngati adzafunika kukucitani opaleshoni kapena kukucitani adimiti, dziŵitsani akulu a mumpingo mwanu pasadakhale. Komanso muyenela kufotokozela acipatala kuti, ngati kwabwela mtumiki wa Mboni za Yehova kudzakuonani ayenela kumulola
Kodi akulu angakuthandizeni bwanji? Akulu angakuthandizeni kulemba khadi la DPA. Komabe, sadzakupangilani cisankho pa nkhani za mankhwala kapena kupeleka maganizo awo pa nkhani za munthu mwini. (Aroma 14:12; Agal. 6:5) Mukadziŵitsa akulu a mumpingo mwanu kuti cithandizo ca mankhwala cimene afuna kukupatsani cingafune magazi, iwo mwamsanga adzadziŵitsa Komiti Yolankhula ndi Acipatala (HLC).
Kodi a HLC angakuthandizeni bwanji? Abale a mu HLC amadziŵa bwino mmene angathandizile acipatala komanso a zamalamulo kumvetsa cikhulupililo cathu pa nkhani ya magazi. Iwo angakambe na madokotala za mankhwala kapena njila zina zothandizila odwala m’malo moika magazi. Pakakhala pofunika, angakuthandizeni kupeza dokotala wogwilizanika.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI KUPANGA CISANKHO PA CITHANDIZO CA CIPATALA COFUNA MAGAZI, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:
Kodi mwaphunzila ciyani mu vidiyo iyi cimene cingakuthandizeni kukonzekela vuto la mwadzidzidzi limene lingabutse nkhani ya magazi?
a Phunzilo 39 m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya lingakuthandizeni popanga zisankho pa nkhani ya cithandizo ca cipatala cimene cingaloŵetsemo magazi.