LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 March tsa. 13
  • Mmene Tingagwilitsile Nchito Mavidiyo Okamba za Phunzilo la Baibo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Tingagwilitsile Nchito Mavidiyo Okamba za Phunzilo la Baibo
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mavidiyo Pophunzitsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Seŵenzetsani Buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Pomanga Cikhulupililo mwa Yehova Komanso mwa Yesu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Seŵenzetsani Mavidiyo Pophunzitsa Anthu Baibo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2019
  • Seŵenzetsani Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mu Ulaliki
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 March tsa. 13
Pogwilitsa nchito tabuleti, mlongo akuonetsa mzimayi vidiyo yakuti “N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?—Yathunthu”.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mmene Tingagwilitsile Nchito Mavidiyo Okamba za Phunzilo la Baibo

Tili na mavidiyo anayi okamba za phunzilo la Baibo amene tingagwilitse nchito mu ulaliki. Kodi iliyonse mwa mavidiyo amenewa inapangidwa na colinga cotani?

  • N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?—Yathunthu. Vidiyo imeneyi inakonzedwa pofuna kuthandiza anthu kukhala na cidwi cophunzila Baibo, mosasamala kanthu kuti amakhulupilila ciyani. Imalimbikitsa anthu kuphunzila Baibo kuti apeze mayankho pa mafunso ofunika kwambili mu umoyo. Ndipo imafotokozako mayankho ena ogwila mtima amene Baibo imapeleka. Imafotokozanso mmene munthu angapemphele phunzilo la Baibo.

  • N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibo? (yaifupi) Mfundo za m’vidiyo imeneyi ni zolingana na zimene zili mu vidiyo yathunthu, koma iyi ni yamphindi imodzi cabe. Ingakhale yothandiza kwambili m’magawo amene anthu amakhala otangwanika.

  • Kodi Phunzilo la Baibo Limacitika Bwanji? Vidiyo imeneyi inakonzedwa kuti izithandiza anthu kukhala na cifuno coyamba kuphunzila nafe Baibo kwaulele. Ndipo imayankha mafunso amene ambili amakhala nawo ponena za Phunzilo la Baibo, kuphatikizapo mmene angapemphele phunzilo.

  • Takulandilani ku Phunzilo Lanu la Baibo. Vidiyo imeneyi inakonzedwa kuti tiziionetsa kwa ophunzila Baibo. Ngakhale kuti vidiyoyi imachulidwa pa tsamba 2 m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, tingaionetse pophunzila bulosha yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Vidiyoyi imafotokoza mwacidule zimene zili m’bukuli, komanso zimene wophunzila angayembekezele pophunzila.

Iliyonse mwa mavidiyo amenewa ili na colinga cake. Komabe, iliyonse tingaionetse kwa anthu kapena kuwatumizila pakakhala pofunikila. Ofalitsa akulimbikitsidwa kuwadziŵa bwino mavidiyo amenewa na kuwagwilitsa nchito mwaluso mu ulaliki.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani