LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 May tsa. 5
  • Kodi Mwakonzeka Kukumana na Mavuto a Zacuma?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Mwakonzeka Kukumana na Mavuto a Zacuma?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Ndimwe Wokonzeka?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Khalanibe Wokonzeka m’Ndime Ino Yothela ya “Masiku Otsiliza”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Kodi Mwakonzekela Kukumana na Zacipolowe?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 May tsa. 5

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mwakonzeka Kukumana na Mavuto a Zacuma?

Nthawi zina zocitika za padzikoli zimayambitsa mavuto a zacuma padziko lonse. Sitidabwa na zimenezi cifukwa tikukhala cakumapeto kwenikweni kwa masiku otsiliza, ndipo Baibo imaticenjeza kuti sitiyenela kudalila “cuma cosadalilika.” (1 Tim. 6:17; 2 Tim. 3:1) Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Mfumu Yehosafati pa nkhani yokonzekela mavuto a zacuma?

Atawopsezedwa na adani, Yehosafati anadalila Yehova. (2 Mbiri 20:9-12) Komanso anakonzekeletsa mtundu wa Yuda mwa kumanga mipanda yolimba kwambili na misasa ya asilikali. (2 Mbiri 17:1, 2, 12, 13) Mofanana na Yehosafati, tiyenela kudalila Yehova na kukonzekela pasadakhale tisanakumane na mavuto.

KODI TINGACITE CIYANI POKONZEKELA MAVUTO A ZACUMA?

Konzekelani mwauzimu: Khalani wokhutila na zimene muli nazo, ndipo limbitsani cidalilo canu cakuti Yehova adzakuthandizani kupeza zofunikila pa umoyo. (Mat. 6:26; 1 Tim. 6:8) Tsimikizani mtima kuti simudzanyalanyaza mfundo za m’Baibo kuti mupeze zofunikila pa umoyo. (Aroma 2:21) Ganizilani mmene mungadzapezele cakudya cauzimu ngati magetsi kapena intaneti kulibe. Sungankoni zofalitsa zosindikizidwa. Ndipo ngati n’zotheka, citani daunilodi pasadakhale zofalitsa za pacipangizo.

Konzekelani kuthupi: Mavuto a zacuma asanayambe, cepetsani nkhongole. Komanso pewani kugula zinthu zosafunikila kwenikweni. (Miy. 22:7) Ngati n’kotheka, sungankoni cakudya cina pambali na zinthu zina zofunikila. Ena amadzilimila ndiwo zamasamba kuti asamawononge ndalama zambili.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KODI MWAKONZEKELA TSOKA LA ZACILENGEDWE? KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

Zithunzi za m’vidiyo yakuti “Kodi Mwakonzekela Tsoka la Zacilengedwe?” Paoneka Baibo, cola cokhala na zofunikila pakagwa tsoka, foni, komanso anchito za mamangidwe.
  • N’ciyani cimene aliyense wa ife angacite pokonzekela tsoka?

Cithunzi ca m’vidiyo yakuti “Kodi Mwakonzekela Tsoka la Zacilengedwe?” Abale othandiza pakagwa tsoka akumanga nyumba na kutsitsa katundu m’thilaki.
  • Kodi tingakonzekele bwanji kuthandiza ena pakagwa tsoka?

COLINGA

Pa kulambila kwa pabanja, kambilanani Galamuka! ya Na. 1 2022. Kambilananinso zina zimene mungacite pokonzekela tsoka.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani