LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 September tsa. 7
  • Abusa Amene Amagwila Nchito Yothandiza Anthu a Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Abusa Amene Amagwila Nchito Yothandiza Anthu a Yehova
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • ‘Itanani Akulu’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Mmene Akulu Amaonetsela Cikondi na Cifundo Kwa Munthu Wocita Chimo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Abale​—Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukayenelele Kukhala Mkulu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 September tsa. 7

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Abusa Amene Amagwila Nchito Yothandiza Anthu a Yehova

Anthu ambili sakhulupilila anthu a paudindo. Ndipo m’pomveka cifukwa kuyambila kale-kale anthu ambili a paudindo akhala akugwilitsa nchito udindo wawo mwadyela. (Mika 7:3) Koma ife ndife oyamikila kwambili kuti akulu mumpingo amaphunzitsidwa kugwilitsa nchito udindo wawo pothandiza anthu a Yehova.—Esitere 10:3; Mat. 20:​25, 26.

Mosiyana na anthu a paudindo a m’dzikoli, abale amayesetsa kuti akhale oyang’anila cifukwa cokonda Yehova na anthu ake. (Yoh. 21:16; 1 Pet. 5:​1-3) Motsogoledwa na Yesu, abusa amenewa amathandiza wofalitsa aliyense kukhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova komanso kudzimva kuti ali m’banja la olambila ake. Iwo sazengeleza kupeleka thandizo lauzimu ku nkhosa za Yehova. Komanso amacitapo kanthu mofulumila ngati wina akufunika thandizo la zacipatala mwamsanga kapena ngati pagwa tsoka linalake. Ngati mufunika thandizo, khalani womasuka kukamba na mkulu aliyense mumpingo mwanu kapena kum’tumila foni.—Yak. 5:14.

Cithunzi ca mu vidiyo yakuti “Abusa Amene Amagwila Nchito Yothandiza Anthu a Yehova.” Mkulu akukumbatila Elias mwacimwemwe popatsana moni.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI AKULU AMENE AMASAMALILA NKHOSA, KENAKO YAKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi Mariana anapindula bwanji na thandizo la akulu?

  • Kodi Elias anapindula bwanji na thandizo la akulu?

  • Pambuyo potamba vidiyoyi, kodi tsopano muiona bwanji nchito imene akulu amagwila?

Kambani na akulu kapena atumileni foni . . .

  • ngati mwasintha kokhala kapena foni namba

  • ngati mukulimbana na ciyeso

  • ngati mudzacokapo kwanthawi yaitali

  • ngati mukufunikila cithandizo camankhwala kapena muli m’cipatala

  • ngati mwacita chimo lalikulu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani